Nebukadinezara alanda Yerusalemu, nalanditsa Yeremiya
1 Chaka chachisanu ndi chinai cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi nkhondo yake yonse kuYerusalemu, ndi kuumangira misasa.
2 Chaka chakhumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai, mzinda unabooledwa.
3 Ndipo akulu onse a mfumu ya ku Babiloni analowa, nakhala m’chipata chapakati, Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu, mkulu wa adindo, Neregali-Sarezare mkulu wa alauli ndi akulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.
4 Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa natuluka m’mzinda usiku, panjira pamunda wa mfumu, pa chipata cha pakati pa makoma awiri; ndipo iye anatulukira panjira ya kuchidikha.
5 Koma nkhondo ya Ababiloni inawalondola, nimpeza Zedekiya m’zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m’dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.
6 Pamenepo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya ku Ribula pamaso pake; mfumu ya ku Babiloni niphanso aufulu onse a Yuda.
7 Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, nammanga m’zigologolo, kunka naye ku Babiloni.
8 Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.
9 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m’mzinda, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am’nsinga ku Babiloni.
10 Koma aumphawi a anthu, amene analibe kanthu, Nebuzaradani kapitao wa alonda anawasiya m’dziko la Yuda, nawapatsa mipesa ndi minda nthawi yomweyo.
11 Ndipo Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anamuuza Nebuzaradani kapitao wa alonda, za Yeremiya, kuti,
12 Umtenge, numyang’anire bwino, usamsautse, koma umchitire monga iye adzanena nawe.
13 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkulu wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Neregali-Sarezere mkulu wa alauli, ndi akulu onse a mfumu ya ku Babiloni;
14 iwonso anatumiza, namchotsa Yeremiya m’bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu.
15 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, potsekeredwa iye m’bwalo la kaidi, kuti,
16 Pita, ukanene kwa Ebedemeleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taona, ndidzafikitsira mzinda uwu mau anga kuusautsa, osauchitira zabwino; ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.
17 Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m’manja a anthu amene uwaopa.
18 Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo sudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nao moyo wako ngati chofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine, ati Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/39-fc60515d9c44e2b7a4f22b8156954c00.mp3?version_id=1068—