Yeremiya achenjeza anthu asapite ku Ejipito
1 Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi Yezaniya mwana wake wa Hosaya, ndi anthu onse kuyambira wamng’ono, kufikira wamkulu, anayandikira,
2 nati kwa Yeremiyamneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m’malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;
3 kuti Yehova Mulungu wanu atisonyeze ife njira imene tiyendemo, ndi chomwe tichite.
4 Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti chilichonse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.
5 Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati sitichita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.
6 Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.
7 Ndipo panali atapita masiku khumi, mau a Yehova anadza kwa Yeremiya.
8 Ndipo anaitana Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu,
9 nati kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, kwa Iye amene munandituma ine ndigwetse pembedzero lanu pamaso pake,
10 Ngati mudzakhalabe m’dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa nacho chisoni choipa chimene ndakuchitirani inu.
11 Musaope mfumu ya ku Babiloni, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndili ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m’dzanja lake.
12 Ndipo ndidzakuchitirani inu chifundo, kuti iye akuchitireni inu chifundo, nakubwezereni inu kudziko lanu.
13 Koma mukati, Sitidzakhala m’dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu;
14 ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;
15 chifukwa chake mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe mu Ejipito, kukakhala m’menemo;
16 pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m’menemo m’dziko la Ejipito, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Ejipito; pamenepo mudzafa.
17 Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Ejipito kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku choipa chimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.
18 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala muYerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.
19 Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe mu Ejipito; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero.
20 Pakuti mwanyenga m’miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita.
21 Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamve mau a Yehova Mulungu wanu m’chinthu chilichonse chimene Iye wanditumira ine nacho kwa inu.
22 Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, komwe mufuna kukakhalako.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/42-c6969a88995b6bfbbdfc609f69f439a7.mp3?version_id=1068—