Amtenga Yeremiya napita naye ku Ejipito
1 Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo,
2 pamenepo ananena Azariya mwana wake wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumize iwe kudzanena, Musalowe mu Ejipito kukhala m’menemo;
3 koma Baruki mwana wake wa Neriya atisonkhezera zoipa za inu, mutipereke m’dzanja la Ababiloni, kuti atiphe ife, atitengere ife am’nsinga ku Babiloni.
4 Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvere mau a Yehova, kuti akhale m’dziko la Yuda.
5 Koma Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera kumitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m’dziko la Yuda;
6 ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya;
7 ndipo anadza nalowa m’dziko la Ejipito; pakuti sanamvere mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.
Yeremiya aneneratu kuti Nebukadinezara adzagonjetsa Ejipito
8 Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yeremiya mu Tapanesi, kuti,
9 Tenga miyala yaikulu m’dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba yaFaraomu Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;
10 ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wake wachifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaivundikira ndi hema wachifumu wake.
11 Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Ejipito; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga.
12 Ndidzayatsa moto m’nyumba za milungu ya Ejipito; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzifunda ndi dziko la Ejipito, monga mbusa avala chovala chake; nadzatuluka m’menemo ndi mtendere.
13 Ndipo adzathyola mizati ya zoimiritsa za Kachisi wa dzuwa, ali m’dziko la Ejipito; ndi nyumba za milungu ya Aejipito adzazitentha ndi moto.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JER/43-30549cf0aa0d720b379d0c2e21ee1ce8.mp3?version_id=1068—