Yeremiya achita nkhawa, adziponya kwa Yehova
1 Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wake.
2 Wanditsogolera, nandiyendetsa mumdima, si m’kuunika ai.
3 Zoonadi amandibwezerabwezera dzanja lake
monditsutsa tsiku lonse.
4 Wagugitsa thupi langa ndi khungu langa,
nathyola mafupa anga.
5 Wandimangira zithando za nkhondo,
wandizinga ndi ulembe ndi mavuto.
6 Wandikhalitsa mumdima ngati akufa kale.
7 Wanditsekereza ndi guta, sindingatuluke;
walemeretsa unyolo wanga.
8 Inde, pofuula ine ndi kuitana andithandize
amakaniza pemphero langa.
9 Watsekereza njira zanga ndi miyala yosema,
nakhotetsa mayendedwe anga.
10 Andikhalira chilombo cholalira kapena mkango mobisalira.
11 Wapambutsa njira zanga, nanding’amba; nandipululutsa.
12 Wathifula uta wake, nandiyesa polozetsa muvi.
13 Walasa impso zanga ndi mivi ya m’phodo mwake.
14 Ndasanduka wondiseka mtundu wanga wonse,
ndi nyimbo yao tsiku lonse.
15 Wandidzaza ndi zowawa, wandikhutitsa chivumulo.
16 Wathyolanso mano anga ndi tinsangalabwi,
wandikuta ndi phulusa.
17 Watalikitsanso moyo wanga ndi mtendere;
ndinaiwala zabwino.
18 Ndipo ndinati, Mphamvu yanga yatha,
osayembekezanso kanthu kwa Yehova.
19 Kumbukirani msauko wanga ndi kusochera kwanga,
ndizo chivumulo ndi ndulu.
20 Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine.
21 Ndili nacho chiyembekezo
popeza ndilingalira ichi ndiyembekeza kanthu.
22 Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova,
pakuti chisoni chake sichileka,
23 chioneka chatsopano m’mawa ndi m’mawa;
mukhulupirika ndithu.
24 Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova;
chifukwa chake ndidzakhulupirira.
25 Yehova akhalira wabwino omlindirira,
ndi moyo womfunafuna.
26 Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha
chipulumutso cha Yehova.
27 Nkokoma kuti munthu asenze goli ali wamng’ono.
28 Akhale pa yekha, natonthole,
pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo.
29 Aike kamwa lake m’fumbi; kapena chilipo chiyembekezo.
30 Atembenuzire wompanda tsaya lake, adzazidwe ndi chitonzo.
31 Pakuti Ambuye sadzataya kufikira nthawi zonse.
32 Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni
monga mwa kuchuluka kwa zifundo zake.
33 Pakuti samasautsa dala,
ngakhale kumvetsa ana a anthu chisoni.
34 Kupondereza andende onse a m’dziko,
35 kupambutsa chiweruzo cha munthu
pamaso pa Wam’mwambamwamba;
36 kukhotetsa mlandu wa munthu, zonsezi Ambuye sazikonda.
37 Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi,
ngati Ambuye salamulira?
38 Kodi m’kamwa mwa Wam’mwambamwamba
simutuluka zovuta ndi zabwino?
39 Kodi munthu wamoyo adandauliranji
pokhala m’zochimwa zake?
40 Tisanthule ntiyese njira zathu ntibwerenso kwa Yehova.
41 Titukulire mitima yathu ndi manja athu omwe
kwa Mulungu ali kumwamba.
42 Ife tilakwa ndi kupikisana nanu,
ndipo Inu simunatikhululukire.
43 Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola,
mwatipha osachitira chisoni.
44 Mwadzikuta ndi mtambo kuti pemphero lathu lisapyolemo.
45 Mwatiika pakati paamitundu
ngati zinyalala ndi za kudzala.
46 Adani athu onse anatiyasamira.
47 Mantha ndi dzenje zitifikira, ndi phokoso ndi chionongeko.
48 M’diso mwanga mutsika mitsinje ya madzi
chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga woonongedwa.
49 Diso langa lingotsanulira osaleka, osapumula,
50 kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona.
51 Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa
chifukwa cha ana aakazi onse a m’mzinda mwanga.
52 Ondida opanda chifukwa anandiinga ngati mbalame;
53 anaononga moyo wanga m’dzenje,
naponya mwala pamwamba pa ine;
54 madzi anayenda pamwamba pamutu panga,
ndinati, Ndalikhidwa.
55 Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndili m’dzenje lapansi;
56 munamva mau anga;
musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine.
57 Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.
58 Ambuye munanenera moyo wanga milandu yake; munaombola moyo wanga.
59 Yehova, mwaona choipa anandichitiracho, mundiweruzire.
60 Mwaona kubwezera kwao konse
ndi zopangira zao zonse za pa ine.
61 Mwamva chitonzo chao, Yehova,
ndi zopangira zao zonse za pa ine,
62 milomo ya akutsutsana nane
ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse.
63 Taonani kukhala ndi kunyamuka kwao; ndine nyimbo yao.
64 Mudzawabwezera chilango, Yehova,
monga mwa machitidwe a manja ao.
65 Muphimbe mtima wao ndi kuwatemberera;
66 mudzawalondola mokwiya
ndi kuwaononga pansi pa thambo la Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LAM/3-c9e87ecdbb892072838aaaf6509216cc.mp3?version_id=1068—