Mtengo wopanda pake
1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, mtengo wampesa uposeranji mtengo uliwonse wina, nthambi ya mpesa yokhalayo mwa mitengo ya kunkhalango?
3 Kodi atengako mtengo kupanga nao ntchito? Atengako chichiri kodi kupachikapo chipangizo chilichonse?
4 Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zake zonse ziwiri, nupserera pakati pake, kodi ukomera ntchito iliyonse?
5 Taonani, pokhala wamphumphu sunayenere ntchito iliyonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso ntchito iliyonse?
6 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala muYerusalemu.
7 Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzatuluka kumoto, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.
8 Ndipo ndidzasandutsa dziko chipululu; popeza anachita cholakwa, ati Ambuye Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/15-b6e0b7a88321e34c615468447e6b148d.mp3?version_id=1068—