Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 26

Za kulangidwa kwa Tiro

1 Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodolaYerusalemu, ndi kuti, Ha! Wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;

3 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Tiro, ndidzakukweretseraamitundu, monga nyanja iutsa mafunde ake.

4 Ndipo adzagumula malinga a Tiro, ndi kugwetsa nsanja zake; inde ndidzausesa fumbi lake, ndi kuuyesa pathanthwe poyera.

5 Udzakhala poyanika khoka pakati pa nyanja, pakuti Ine ndachinena, ati Ambuye Yehova; ndipo udzakhala chofunkha cha amitundu.

6 Ndi ana ake aakazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

7 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Tiro Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mfumu ya mafumu, yochokera kumpoto ndi akavalo, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri.

8 Ana ako aakazi adzawapha kumunda ndi lupanga; ndipo adzakumangira nsanja, ndi kukuundira mtumbira, ndi kukuimikira chikopa.

9 Nadzaikira malinga ako zogumulira, nadzagwetsa nsanja zako ndi zida zake.

10 Popeza achuluka akavalo ake, fumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magaleta, polowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m’mzinda popasukira linga lake.

11 Ndi ziboda za akavalo ake iye adzapondaponda m’makwalala ako onse; adzapha anthu ako ndi lupanga; ndi zoimiritsa za mphamvu yako zidzagwa pansi.

12 Ndipo adzalanda chuma chako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi fumbi lako, m’madzi.

13 Ndipo ndidzaleketsa phokoso la nyimbo zako, ndi kulira kwa mazeze ako sikudzamvekanso.

14 Ndipo ndidzakuyesa pathanthwe poyera; udzakhala poyanika khoka, sadzakumanganso; pakuti Ine Yehova ndachinena, ati Ambuye Yehova.

15 Atero Ambuye Yehova kwa Tiro, Zisumbu sizidzagwedezeka nanga pomveka kugwa kwako, pobuula olasidwa, pakuchitika kuphako pakati pako?

16 Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yachifumu yao, nadzavula zovala zao zopikapika, nadzavala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kudabwa nawe.

17 Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pokhala pa anthu a panyanja, mzinda womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo!

18 Pamenepo zisumbu zidzanjenjemera tsiku la kugwa kwako, inde zisumbu za kunyanja zidzatenga nkhawa pa kuchokera kwako.

19 Pakuti atero Ambuye Yehova, Pamene ndikusandutsa mzinda wopasuka, ngati mizinda yosakhalamo anthu, ndi kukukweretsera nyanja, nadzakumiza madzi aakulu;

20 pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m’dziko la amoyo,

21 ndidzakuika woopsa; ndipo sudzaonekanso, chinkana akufunafuna sudzapezekanso konse, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/26-04c1a8181cb6af7962f31e979ed5dd0d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *