Aneneratu motsutsa abusa osakhulupirika a anthu a Mulungu
1 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?
3 Mukudya mafuta, muvala ubweya, mukupha zonenepa; koma simudyetsa nkhosa.
4 Zofooka simunazilimbitse; yodwala simunaichiritse, yothyoka simunailukire chika, yopirikitsidwa simunaibweze, yotayika simunaifune; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa.
5 M’mwemo zinamwazika posowa mbusa, ndipo zinakhala chakudya cha zilombo zilizonse zakuthengo, popeza zinamwazika.
6 Nkhosa zanga zinasokera kumapiri ali onse, ndi pa chitunda chilichonse chachitali; inde nkhosa zanga zinabalalika padziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.
7 Chifukwa chake abusa inu, imvani mau a Yehova:
8 Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakuthengo, chifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunefune nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;
9 chifukwa chake, abusa inu, imvani mau a Yehova:
10 Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga padzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzachitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale chakudya chao.
11 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.
12 Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m’malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.
13 Ndipo ndidzazitulutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m’maiko, ndi kulowa nazo m’dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israele, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m’dziko.
14 Ndidzazidyetsa podyetsa pabwino; ndi pa mapiri aatali a Israele padzakhala kholo lao, apo adzagona m’khola mwabwino, nadzadya podyetsa pokometsera pa mapiri a Israele.
15 Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa, ati Ambuye Yehova.
16 Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
17 Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.
18 Kodi chikucheperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? Muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? Muyenera kumwa madzi odikha, ndi kuvundulira otsalawo ndi mapazi anu?
19 Ndi nkhosa zanga zidye kodi zoponderezeka ndi mapazi anu, ndi kumwa zovunduliridwa ndi mapazi anu?
20 Chifukwa chake atero nao Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzaweruza pakati pa zoweta zonenepa, ndi zoweta zoonda.
21 Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,
22 chifukwa chake ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso chakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta.
23 Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.
24 Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.
25 Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m’dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m’chipululu, ndi kugona kunkhalango.
26 Pakuti ndidzaika izi ndi midzi yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m’nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso.
27 Ndi mitengo yakuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m’dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m’manja mwa iwo akuwatumikiritsa.
28 Ndipo sadzakhalanso chakudya chaamitundu, ndi chilombo chakuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.
29 Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzachotsedwanso ndi njala m’dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.
30 Ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wao ndili nao, ndi kuti iwo, nyumba ya Israele, ndiwo anthu anga, ati Ambuye Yehova.
31 Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/34-94f4aa5fb41523cccc67caa521ae4650.mp3?version_id=1068—