Kukonzekanso kwa Kachisi: malo opatulika kwambiri
1 Ndipo anadza nane ku Kachisi, nayesa nsanamira zake, kupingasa kwake mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko, ndiko kupingasa kwa chihema chija.
2 Ndi kupingasa kwa khomo mikono khumi; ndi mbali za khomo mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; nayesa malo opatulika, m’litali mwake mikono makumi anai, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.
3 Nalowa m’katimo, nayesa mphuthu za pakhomo mikono iwiri, ndi msinkhu wa khomo mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwa khomo mikono isanu ndi iwiri.
4 Anayesanso m’kati mwa Kachisi m’tsogolomo, m’litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m’mopatulika kwambiri.
5 Pamenepo anayesa khoma la nyumba, kuchindikira kwake mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwake kwa zipinda za m’mphepete mikono inai, pozungulira pake ponse pa Kachisi.
6 Ndipo zipinda za m’mphepete zinasanjikizana china pa chinzake; zinatero makumi atatu mizere yonse itatu, ndipo zinalowa kukhoma lochirikiza zipinda za m’mphepete pozungulirapo, zisanjikike pamenepo; pakuti sizinagwiridwe ndi khoma la nyumba.
7 Ndipo zipinda za m’mphepete zinakula m’kupingasa kwao, pozinga nyumba m’kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pake pa nyumba; motero kupingasa kwake kwa nyumba kunakula kumwamba kwake, momwemonso anakwera kuyambira chipinda chakunsi, kupita chapakati, kufikira cham’mwamba.
8 Ndinaonanso kuti kunyumba kunali chiunda pozungulira pake; maziko a zipinda za m’mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikulu.
9 Kuchindikira kwa khoma la kuzipinda za m’mphepete kunja kwake kunali mikono isanu; ndipo mpata wake unali malo olowera m’zipinda za m’mphepete za Kachisi.
10 Ndi pakati pa zipinda panali kupingasa kwa mikono makumi awiri, pozungulira pake ponse pa nyumba.
11 Ndi makomo a zipinda za m’mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwera; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwake pozungulira pake.
12 Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwake; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pake linali la mikono isanu kuchindikira kwake; ndi m’litali mwake mikono makumi asanu ndi anai.
13 Momwemo anayesa Kachisi m’litali mwake mikono zana limodzi; ndi mpatawo, ndi nyumbayo, ndi makoma ake, mikono zana limodzi;
14 kupingasa kwake komwe kwa kukhomo kwa nyumba, ndi kumpatawo kum’mawa, mikono zana limodzi.
15 Momwemo anayesa m’litali mwake nyumbayo inali kutsogolo kwake kwa mpata wokhala chakuno chake, ndi makonde ake am’mwamba, chakuno ndi chauko, mikono zana limodzi, ndi Kachisi wa m’katimo, ndi makonde a kubwalo;
16 ziundo, ndi mazenera amkati okhazikika, ndi makonde am’mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa chiundo, otchinga ndi matabwa pozungulira pake, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika;
17 kufikira kumwamba pa khomo, mpaka nyumba ya m’katimo, ndi kunja kwake, ndi khoma lonse kwete m’kati ndi kunja, monga mwa miyeso.
18 Ndipo panalembedwapo ndiakerubindi akanjedza, kanjedza pakati pa akerubi; ndi kerubi aliyense anali ndi nkhope zake ziwiri;
19 nkhope ya munthu kuloza kukanjedza chakuno, ndi nkhope ya mwanawamkango kuloza kukanjedza chauko, momwemo m’nyumba monse pozungulira pake.
20 Kuyambira pansi kufikira pamwamba pa khomo panalembedwa akerubi ndi akanjedza; linatero khoma la Kachisi.
21 Mphuthu za Kachisi zinali zaphwamphwa, ndi maonekedwe a pakhomo pa malo opatulika ananga maonekedwe a Kachisi.
22 Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m’litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova.
23 Ndipo Kachisi ndi malo opatulika kwambiri anali nazo zitseko ziwiri.
24 Ndipo pamakomopo panali zitseko zopatukana zotembenuzika, china chopatukana pa khomo lina china pa linzake.
25 Ndipo panalembedwa pamenepo pa zitseko za Kachisi akerubi ndi akanjedza, akunga aja adalembedwa pamakoma; ndipo panali matabwa ochindikira pakhomo pakhonde panja.
26 Ndipo panali mazenera amkati okhazikika, ndi akanjedza chakuno ndi chauko, kumbali zake za khonde; momwemonso pa zipinda za m’mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ochindikira.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/41-4de6676b8abb8d904adf0a2941a37301.mp3?version_id=1068—