Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 44

Kukonzekanso kwa Kachisi utumiki wa Alevi ndi ansembe

1 Pamenepo anandibweza njira ya kuchipata chakunja cha malo opatulika choloza kum’mawa, koma chinatsekedwa.

2 Ndipo Yehova anati kwa ine, Chipata ichi chitsekeke, chisatseguke, osalowako munthu; pakuti Yehova Mulungu wa Israele walowerapo; chifukwa chake chitsekeke.

3 Koma kunena za kalonga, iye akhale m’menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe kunjira ya kukhonde la chipata, natulukire njira yomweyi.

4 Atatero anamuka nane njira ya chipata cha kumpoto kukhomo kwa Kachisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi.

5 Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m’makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ake onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi matulukidwe ake onse a malo opatulika.

6 Nunene kwa opandukawo, kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Nyumba ya Israele inu, Zikukoleni zonyansa zanu zonse;

7 popeza mwalowa nao achilendo osadulidwa m’mtima, osadulidwa m’thupi akhale m’malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munathyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.

8 Ndipo simunasunge udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira nokha osunga udikiro wanga m’malo anga opatulika.

9 Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m’mtima, wosadulidwa m’thupi, alowe m’malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israele.

10 Koma Aleviwo anandichokera kunka kutaliwo, posokera Israele, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao.

11 Koma adzakhala atumiki m’malo anga opatulika, akuyang’anira kuzipata za Kachisi, ndi kutumikira mu Kachisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera, naime pamaso pao kuwatumikira.

12 Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala chokhumudwitsa cha mphulupulu cha nyumba ya Israele, chifukwa chake ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao.

13 Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira ntchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga zilizonse zopatulika kwambirizo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazichita.

14 Koma ndidzawaika akhale osunga udikiro wa Kachisi kwa utumiki wake wonse, ndi zonse zakumachitika m’mwemo.

15 Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israele, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;

16 iwowa adzalowa m’malo anga opatulika, nadzayandikira kugome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga.

17 Ndipo kudzatero, polowa iwo kuzipata za bwalo lam’kati avale zovala zabafuta; koma zaubweya asazivale ponditumikira Ine m’zipata za bwalo la m’kati, ndi mu Kachisi.

18 Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m’chuuno mwao; asavale m’chuuno kanthu kalikonse kakuchititsa thukuta.

19 Ndipo akatulukira kubwalo lakunja, kubwalo lakunja kuli anthu, azivula zovala zao zimene atumikira nazo, naziike m’zipinda zopatulika, navale zovala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.

20 Ndipo asamete mitu yao, kapena asalekerere nzera za tsitsi lao zikule, azingoyepula tsitsi la mitu yao.

21 Kungakhale kumwa vinyo, wansembe asamwe polowa kubwalo la m’katimo.

22 Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asachite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israele, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.

23 Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.

24 Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pazikondwerero zanga zonse zoikika; napatulikitsemasabataanga.

25 Ndipo asayandikire kwa munthu aliyense wakufa, angadzidetse; koma chifukwa cha atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.

26 Ndipo atayeretsedwa amwerengere masiku asanu ndi awiri.

27 Ndipo tsiku loti alowa m’malo opatulika, bwalo lam’kati, kutumikira m’malo opatulika, apereke nsembe yake yauchimo, ati Ambuye Yehova.

28 Ndipo adzakhala nacho cholowa; Ine ndine cholowa chao; musawapatsa cholandira chao mu Israele; Ine ndine cholandira chao.

29 Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zao.

30 Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zilizonse, ndi nsembe zokweza zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.

31 Ansembe asadyeko kanthu kakufa kokha, kapena kogwidwa ndi chilombo, ngakhale mbalame, kapena nyama.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/44-c3408ef48043d94f88e9515dd8fa00ed.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *