Categories
DANIELE

DANIELE 2

Nebukadinezara alota, Daniele ammasulira lotolo

1 Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira.

2 Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Ababiloni, amuululire mfumu maloto ake. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu.

3 Niti nao mfumu, Ndalota loto, nuvutika mzimu wanga kudziwa lotolo.

4 Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu mu Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake.

5 Niyankha mfumu, niti kwa Ababiloni, Chandichokera chinthuchi; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala.

6 Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwake, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukulu; chifukwa chake mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwake.

7 Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ake lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwake.

8 Mfumu inayankha, niti, Ndidziwatu kuti mukunkhuniza dala, pakuona inu kuti chinthuchi chandichokera.

9 Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; chifukwa chake mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwake komwe.

10 Ababiloni anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu padziko lapansi wokhoza kuwulula mlandu wa mfumu; chifukwa chake palibe mfumu, mkulu, kapena wolamulira, wafunsira chinthu chotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Ababiloni ali onse.

11 Pakuti chinthu achifuna mfumu nchapatali; ndipo palibe wina wokhoza kuchiwulula pamaso pa mfumu, koma milungu imene kwao sikuli pamodzi ndi anthu.

12 Chifukwa chake mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse mu Babiloni.

13 M’mwemo chilamulirocho chidamveka, ndi eni nzeru adati aphedwe; anafunafunanso Daniele ndi anzake aphedwe.

14 Pamenepo Daniele anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, adatulukawo kukapha eni nzeru a ku Babiloni;

15 anayankha nati kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, Chilamuliro cha mfumu chifulumiriranji? Pamenepo Ariyoki anadziwitsa Daniele chinthuchi.

16 Nalowa Daniele, nafunsa mfumu amuikire nthawi, kuti aululire mfumu kumasulira kwake.

17 Pamenepo Daniele anapita kunyumba kwake, nadziwitsa anzake Hananiya, Misaele, ndi Azariya, chinthuchi;

18 kuti apemphe zachifundo kwa Mulungu wa Kumwamba pa chinsinsi ichi; kuti Daniele ndi anzake asaonongeke pamodzi ndi eni nzeru ena a ku Babiloni.

19 Pamenepo chinsinsicho chinavumbulutsidwa kwa Daniele m’masomphenya a usiku. Ndipo Daniele analemekeza Mulungu wa Kumwamba.

20 Daniele anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu kunthawi za nthawi, pakuti nzeru ndi mphamvu zili zake;

21 pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.

22 Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.

23 Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.

24 Potero Daniele analowa kwa Ariyoki amene mfumu idamuika aononge eni nzeru a ku Babiloni; anamuka, natero naye, Usaononga eni nzeru a ku Babiloni, undilowetse kwa mfumu, ndipo ndidzaululira mfumu kumasulirako.

25 Pamenepo Ariyoki analowa naye Daniele kwa mfumu mofulumira; natero nayo, Ndapeza munthu wa ana a ndende a Yuda, ndiye adzadziwitsa mfumu kumasulira kuja.

26 Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, amene dzina lake ndiye Belitesazara, Ukhoza kodi kundidziwitsa lotolo ndidalilota, ndi kumasulira kwake?

27 Nayankha Daniele pamaso pa mfumu, nati, Chinsinsi inachitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sangathe kuchiululira mfumu;

28 koma kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m’mtima mwanu pakama panu, ndi awa:

29 Inu mfumu, maganizo anu analowa m’mtima mwanu muli pakama panu, akunena za icho chidzachitika m’tsogolomo; ndipo Iye amene avumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani chodzachitikacho.

30 Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwe kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.

31 Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikulu. Fanoli linali lalikulu, ndi kunyezimira kwake kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ake anali oopsa.

32 Fano ili tsono, mutu wake unali wagolide wabwino, chifuwa chake ndi manja ake zasiliva, mimba yake ndi chuuno chake zamkuwa,

33 miyendo yake yachitsulo, mapazi ake mwina chitsulo mwina dongo.

34 Munali chipenyere kufikira mwala unasemedwa popanda manja, umene unagunda fanoli pa mapazi ake okhala chitsulo ndi dongo, nuwaphwanya.

35 Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golide, zinapereka pamodzi, ndipo zinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi.

36 Ili ndi loto; kumasulira kwake tsono tikufotokozerani mfumu.

37 Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wa Kumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemu;

38 ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama zakuthengo, ndi mbalame za m’mlengalenga, m’dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide.

39 Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu, ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu padziko lonse lapansi.

40 Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa.

41 Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zake, mwina dongo la woumba, mwina chitsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya chitsulo; popeza mudaona chitsulo chosakanizika ndi dongo.

42 Ndi zala za mapazi, mwina chitsulo ndi mwina dongo, momwemo ufumuwo, mwina wolimba mwina wogamphuka.

43 Ndi umo mudaonera chitsulo chosakanizika ndi dongo, iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma sadzaphatikizana, monga umo chitsulo sichimasakanizikana ndi dongo.

44 Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.

45 Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m’phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m’tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika.

46 Pamenepo mfumu Nebukadinezara anagwa nkhope yake pansi, nalambira Daniele, nati amthirire nsembe yaufa ndi ya zonunkhira zokoma.

47 Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi.

48 Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.

49 Pamenepo Daniele anapempha mfumu, ndipo anaika Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ayang’anire ntchito za dera la ku Babiloni. Koma Daniele anakhala m’bwalo la mfumu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/2-903d3415070c68b9b78d917b294b1e90.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *