Categories
DANIELE

DANIELE 3

Nebukadinezara apanga fano lagolide

1 Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolide, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lake mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa chidikha cha Dura, m’dera la ku Babiloni.

2 Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwere kuzulula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara.

3 Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara.

4 Ndipo wolalikira anafuulitsa, kuti, Akulamulirani inu anthu, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana,

5 kuti pakumva inu mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara;

6 ndipo aliyense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m’kati mwa ng’anjo yotentha yamoto.

7 Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi zoimbitsa zilizonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara.

8 Chifukwa chake anayandikira Ababiloni ena nthawi yomweyi, naneneza Ayuda.

9 Anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire.

10 Inu mfumu mwalamulira kuti munthu aliyense amene adzamva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, agwadire, nalambire fanolo lagolide;

11 ndi yense wosagwadira ndi kulambira adzaponyedwa m’kati mwa ng’anjo yotentha yamoto.

12 Alipo Ayuda amene munawaika ayang’anire ntchito ya dera la ku Babiloni, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amuna awa, mfumu, sanasamalire inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.

Anzake a Daniele aponyedwa m’ng’anjo yamoto

13 Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi mu ukali wake, anawauza abwere nao Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.

14 Nebukadinezara anayankha, nati kwa iwo, Kodi mutero dala, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, kusatumikira milungu yanga, ndi kusalambira fano lagolide ndinaliimikalo?

15 Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m’kati mwa ng’anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu yemwe adzakulanditsani m’manja mwanga ndani?

16 Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu.

17 Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m’ng’anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m’dzanja lanu, mfumu.

18 Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.

19 Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anasandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng’anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.

20 Nauza amuna ena amphamvu a m’khamu lake la nkhondo amange Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ndi kuwaponya m’ng’anjo yotentha yamoto.

21 Pamenepo amuna awa anamangidwa ali chivalire zofunda zao, malaya ao, ndi nduwira zao, ndi zovala zao zina; naponyedwa m’kati mwa ng’anjo yotentha yamoto.

22 Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng’anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego.

23 Ndipo amuna atatu awa, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anagwa pansi omangidwa m’kati mwa ng’anjo yotentha yamoto.

24 Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ake, Kodi sitinaponye amuna atatu omangidwa m’kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu.

25 Anayankha, nati, Taonani, ndilikuona amuna anai omasuka, alikuyenda m’kati mwa moto; ndipo alibe kuphwetekwa, ndi maonekedwe a wachinai akunga mwana wa milungu.

26 Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo la ng’anjo yotentha yamoto, analankhula, nati, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, inu atumiki a Mulungu Wam’mwambamwamba, tulukani, idzani kuno. Pamenepo Sadrake, Mesake, ndi Abedenego, anatuluka m’kati mwa moto.

27 Ndipo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, ndi mandoda a mfumu, atasonkhana, anaona amuna awa, kuti moto unalibe mphamvu pa matupi ao, losawauka tsitsi la pamutu pao, ndi zofunda zao zosasandulika, fungo lomwe lamoto losawaomba.

28 Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.

29 Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.

30 Pamenepo mfumu inakuza Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, m’dera la ku Babiloni.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/3-36d3dcc9ef3cc11b8ec5ddbe136c7672.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *