Categories
DANIELE

DANIELE 6

Akalonga amtchulira Daniele chifukwa kwa Dariusi

1 Kudamkomera Dariusi kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m’madera onse a ufumu;

2 ndi akuyang’anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Daniele; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke.

3 Pamenepo Daniele amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang’anira ufumu wonse.

4 Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.

5 Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola chifukwa chilichonse Daniele amene, tikapanda kumtola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake.

6 Ndipo akulu awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariusi, mukhale ndi moyo chikhalire.

7 Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m’dzenje la mikango.

8 Tsopano, mfumu, mukhazikitse choletsacho, ndi kutsimikiza cholembedwacho, kuti chisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika.

9 Momwemo mfumu Dariusi anatsimikiza cholembedwa ndi choletsacho.

10 Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m’nyumba mwake, m’chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza kuYerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.

11 Pamenepo anasonkhana anthu awa, napeza Daniele alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wake.

12 Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za choletsacho cha mfumu, Kodi simunatsimikize choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m’dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.

13 Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Daniele uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena choletsa munachitsimikizacho; koma apempha pemphero lake katatu tsiku limodzi.

14 Ndipo mfumu m’mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wake pa Daniele kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.

15 Koma anthu awa anasonkhana kwa mfumu, nati kwa mfumu, Dziwani, mfumu, kuti lamulo la Amedi ndi Aperisi, ndilo kuti choletsa chilichonse ndi lemba lililonse idazikhazikira mfumu, zisasinthike.

Daniele aponyedwa m’dzanja la mikango

16 Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m’dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.

17 Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi chosindikizira chake, ndi chosindikizira cha akulu ake, kuti kasasinthike kanthu ka Daniele.

18 Pamenepo mfumu inamuka kuchinyumba chake, nichezera kusala usikuwo, ngakhale zoimbitsa sanabwere nazo pamaso pake, ndi m’maso mwake munamuumira.

19 Nilawira mamawa mfumu, nimuka mofulumira kudzenje la mikango.

20 Ndipo poyandikira padzenje inafuula ndi mau achisoni mfumu, ninena, niti kwa Daniele, Daniele, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango?

21 Pamenepo Daniele anati kwa mfumu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire.

22 Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.

23 Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza atulutse Daniele m’dzenje. Momwemo anamtulutsa Daniele m’dzenje, ndi pathupi pake sipadaoneke bala, popeza anakhulupirira Mulungu wake.

24 Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m’dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.

25 Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala padziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu.

26 Ndilamulira ine kuti m’maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro.

27 Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m’mwamba ndi padziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango.

28 Momwemo Daniele amene anakuzikabe pokhala Dariusi mfumu, ndi pokhala mfumu Kirusi wa ku Persiya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/6-981d7959016bac1e1deaa649561e5716.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *