Hoseya akwatira mkazi woipa kufanizira zoipa za Israele
1 Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.
2 Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova.
3 Ndipo anamuka natenga Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu; iye naima, nambalira mwana wamwamuna.
4 Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele.
5 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzathyola uta wa Israele m’chigwa cha Yezireele.
6 Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Wosachitidwa-chifundo; pakuti sindidzachitiranso chifundo nyumba ya Israele, kuti ndiwakhululukire konse.
7 Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.
8 Ataleka tsono kuyamwitsa Wosachitidwa-chifundo, anaima, nabala mwana wamwamuna.
9 Ndipo Yehova anati, Umutche dzina lake Si-anthu-anga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.
Israele achitidwa chifundo
10 Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m’mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.
11 Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israele adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkulu mmodzi, nadzakwera kuchoka m’dziko; pakuti tsiku la Yezireele ndi lalikulu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/1-474d1109dd4267da8fd348ea812427af.mp3?version_id=1068—