1 Nenani kwa abale anu, Anthu anga, ndi kwa alongo anu, Wochitidwa-chifundo.
2 Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindili mwamuna wake; ndipo achotse zadama zake pankhope pake, ndi zigololo zake pakati pa mawere ake;
3 ndingamvule wamaliseche, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati chipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;
4 ndipo ana ake sindidzawachitira chifundo; pakuti iwo ndiwo ana achigololo.
5 Pakuti mai wao anachita chigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anachita chamanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine chakudya changa, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi chakumwa changa.
6 Chifukwa chake taonani, ndidzatchinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ake.
7 Ndipo adzatsata omkonda koma osawagwira, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano.
8 Pakuti sanadziwe kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsirasilivandi golide, zimene anapanga nazoBaala.
9 Chifukwa chake ndidzabwera ndi kuchotsa tirigu wanga m’nyengo yake, ndi vinyo wanga m’nthawi yake yoikika, ndi kukwatula ubweya wanga ndi thonje langa, zimene zikadafunda umaliseche wake.
10 Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ake pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m’dzanja langa.
11 Ndidzaleketsanso kusekerera kwake konse, zikondwerero zake, pokhala mwezi pake, ndimasabataake, ndi misonkhano yake yonse yoikika.
12 Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.
13 Ndipo ndidzamlanga chifukwa cha masiku a Abaala amene anawafukizira, navala mphete za m’mphuno, ndi zokometsera zake, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova.
14 Chifukwa chake taonani, ndidzamkopa ndi kunka naye kuchipululu, ndi kulankhula naye momkonda mtima.
15 Ndipo ndidzampatsa minda yake yampesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m’dziko la Ejipito.
16 Ndipo kudzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, udzanditcha Mwamuna wanga, osanditchanso Baala wanga.
17 Pakuti ndidzachotsa maina a Abaala m’kamwa mwake; ndipo silidzakumbukikanso dzina lao.
18 Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m’dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.
19 Ndipo ndidzakutomera ukhale wanga kosatha, inde ndidzakutomera ukhale wanga m’chilungamo, ndi m’chiweruzo, ndi mu ukoma mtima, ndi m’chifundo.
20 Ndidzakutomeranso ukhale wanga mokhulupirika, ndipo udzadziwa Yehova.
21 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzavomereza, ati Yehova, ndidzavomereza thambo, ndi ilo lidzavomereza dziko lapansi;
22 ndi dziko lapansi lidzavomereza tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndi izi zidzavomereza Yezireele.
23 Ndipo ndidzadzibzalira iye m’nthaka, ndipo ndidzachitira chifundo Wosachitidwa-chifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/2-d0827379effc90ec6a2ca243d99ab6a3.mp3?version_id=1068—