Kulowerera kwa Israele
1 Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.
2 Ndipo opandukawo analowadi m’zovunda; koma Ine ndine wakuwadzudzula onsewo.
3 Ndimdziwa Efuremu, ndi Israele sandibisikira; pakuti Efuremu iwe, wachita uhule tsopano, Israele wadetsedwa.
4 Machitidwe ao sawalola kubwerera kwa Mulungu wao; pakuti mzimu wa uhule uli m’kati mwao, ndipo sadziwa Yehova.
5 Ndipo kudzikuza kwa Israele kudzamchitira umboni pamaso pake; chifukwa chake Israele ndi Efuremu adzakhumudwa m’mphulupulu mwao; Yudanso adzakhumudwa pamodzi nao.
6 Adzamuka ndi zoweta zao zazing’ono ndi zazikulu kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwachokera.
7 Anachita mosakhulupirika pa Yehova, pakuti anabala ana achilendo; mwezi wokhala udzawatha tsopano, pamodzi ndi maiko ao.
8 Ombani mphalasa mu Gibea, ndi lipenga mu Rama; fuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini.
9 Efuremu adzasanduka bwinja tsiku lakudzudzula; mwa mafuko a Israele ndadziwitsa chodzachitikadi.
10 Akalonga a Yuda akunga anthu osuntha malire; ndidzawatsanulira mkwiyo wanga ngati madzi.
11 Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo.
12 Ndipo ndikhala kwa Efuremu ngati njenjete, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati chivundi.
13 Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu.
14 Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.
15 Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m’msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/5-69ac92977b370130c45d0a23147dca4e.mp3?version_id=1068—