Israele abwerera kunka kwa Yehova
1 Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang’amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.
2 Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.
3 Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.
Efuremu ndi Yuda adzudzulidwa
4 Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam’mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.
5 Chifukwa chake ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga atuluka ngati kuunika.
6 Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.
7 Koma iwo analakwirachipanganongati Adamu, m’mene anandichitira monyenga.
8 Giliyadi ndiwo mzinda wa ochita zoipa, wa mapazi a mwazi.
9 Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha panjira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa.
10 M’nyumba ya Israele ndinaona chinthu choopsetsa; pamenepo pali uhule wa Efuremu; Israele wadetsedwa.
11 Akuikidwiratunso nyengo yakukolola, Yuda iwe, pamene ndikabwezanso undende wa anthu anga.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/6-91f08a560cb7983efa0c21a59fae79af.mp3?version_id=1068—