Aneneratu za chilango cha Mulungu pa adani ake; Israele adzakonzekanso
1 Pakuti taonani, masiku awo, ndi nthawi iyo, pamene ndibwera nao andende a Yuda ndi aYerusalemu,
2 ndidzasonkhanitsaamitunduonse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa.
3 Ndipo anachitira anthu anga maere, napereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe.
4 Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Filistiya? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu.
5 Popeza inu munatengasilivawanga ndi golide wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma mu akachisi anu;
6 munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwachotsa kutali kwa malire ao;
7 taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera chilango chanu pamutu panu;
8 ndipo ndidzagulitsa ana ako aamuna ndi aakazi m’dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutali; pakuti Yehova wanena.
9 Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.
10 Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi zikwakwa zanu zikhale nthungo; wofooka anene, Ndine wamphamvu.
11 Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi, mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova.
12 Agalamuke amitundu, nakwerere kuchigwa cha Yehosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira.
13 Longani chisenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikulu.
14 Aunyinji, aunyinji m’chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m’chigwa chotsirizira mlandu.
15 Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao.
16 Ndipo Yehova adzadzuma ali kuZiyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.
17 Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,
18 Ndipo kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m’mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi akasupe adzatuluka m’nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu.
19 Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m’dziko lao.
20 Koma Yuda adzakhala chikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwomibadwo.
21 Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala mu Ziyoni.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOL/3-13f23c99e02b5a637d29036cec975688.mp3?version_id=1068—