Categories
1 YOHANE

1 YOHANE 2

1 Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye YesuKhristuwolungama;

2 ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.

Za kusunga malamulo, kukondana, ndi kudzimana zapadziko

3 Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake.

4 Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;

5 koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M’menemo tizindikira kuti tili mwa Iye;

6 iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo.

7 Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa chiyambi; lamulo lakalelo ndilo mau amene mudawamva.

8 Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chili choona mwa Iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala.

9 Iye amene anena kuti ali m’kuunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino.

10 Iye amene akonda mbale wake akhala m’kuunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.

11 Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.

12 Ndikulemberani, tiana, popeza machimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lake.

13 Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.

14 Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamgonjetsa woipayo.

15 Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye.

16 Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.

17 Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.

Za okana Khristu

18 Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.

19 Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.

20 Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.

21 Sindinakulembereni chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi.

22 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana.

23 Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wovomereza Mwana ali ndi Atatenso.

24 Koma inu, chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala mwa inu chimene mudachimva kuyambira pachiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate.

25 Ndipo ili ndi lonjezano Iye anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha.

26 Izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu.

27 Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.

28 Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa Iye; kuti akaonekere Iye tikakhale nako kulimbika mtima, osachita manyazi kwa Iye pa kudza kwake.

29 Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1JN/2-705d454469123994948e9f5864b31ebc.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *