Categories
1 YOHANE

1 YOHANE 3

Ife ndife ana a Mulungu

1 Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.

2 Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.

3 Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.

4 Yense wakuchita tchimo achitanso kusaweruzika; ndipo tchimo ndilo kusaweruzika.

5 Ndipo mudziwa kuti Iyeyu anaonekera kudzachotsa machimo; ndipo mwa Iye mulibe tchimo.

6 Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuone Iye, ndipo sanamdziwe Iye.

7 Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakuchita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama:

8 iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.

9 Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sangathe kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.

10 M’menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.

11 Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake:

12 osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.

13 Musazizwe, abale, likadana nanu dziko lapansi.

14 Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka muimfa kulowa m’moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda akhala muimfa.

15 Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.

16 Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.

17 Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?

18 Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’choonadi.

19 Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m’choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake,

20 m’mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.

21 Okondedwa, mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa Mulungu;

22 ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.

23 Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake YesuKhristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga anatilamulira.

24 Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m’menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1JN/3-fcb9d35c2182c7c442dcd528bb0d9b42.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *