Pemphero la Yona ali m’mimba mwa chinsomba
1 Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake ali m’mimba mwa nsombayo.
2 Ndipo anati,
Ndinaitana Yehova m’nsautso wanga,
ndipo anandiyankha ine;
ndinafuula ndili m’mimba ya manda,
ndipo munamva mau anga.
3 Pakuti munandiponya mwakuya m’kati mwa nyanja,
ndipo madzi anandizinga;
mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
4 Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu;
koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika.
5 Madzi anandizinga mpaka moyo wanga,
madzi akuya anandizungulira,
kayandeyande wa m’nyanja anandikulunga mutu.
6 Ndinatsikira kumatsinde a mapiri,
mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha;
koma munandikwezera moyo wanga
kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.
7 Pokomoka moyo wanga m’kati mwanga ndinakumbukira Yehova;
ndi pemphero langa linafikira Inu mu Kachisi wanu wopatulika.
8 Iwo osamalira mabodza opanda pake
ataya chifundo chaochao.
9 Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika,
ndidzakwaniritsa chowinda changa.
Chipulumutso ncha Yehova.
10 Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JON/2-58e99d0de00220c8f33c33195a6f9d77.mp3?version_id=1068—