Mau akudzudzula Yerusalemu. Malonjezo a kwa okhulupirika otsala
1 Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mzinda wozunza!
2 Sanamvera mau, sanalole kulangizidwa; sanakhulupirire Yehova, sanayandikire kwa Mulungu wake.
3 Akalonga ake m’kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.
4 Aneneri ake ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe ao anaipsa malo opatulika, napotoza chilamulo.
5 Yehova pakati pake ali wolungama; sadzachita chosalungama, m’mawa ndi m’mawa aonetsera chiweruzo chake poyera, chosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.
6 Ndaonongaamitundu; nsanja zao za kungodya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; mizinda yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.
7 Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pake pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, navunditsa machitidwe ao onse.
8 Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.
9 Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.
10 Kuchokera tsidya lija la mitsinje ya Kusi ondipembedza, ndiwo mwana wamkazi wa obalalika anga, adzabwera nacho chopereka changa.
11 Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m’phiri langa lopatulika.
12 Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.
13 Otsala a Israele sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m’kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.
14 Imba, mwana wamkazi waZiyoni; fuula, Israele; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi waYerusalemu.
15 Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israele, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso choipa.
16 Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka.
17 Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m’chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.
18 Ndidzasonkhanitsa iwo akulirira msonkhano woikika, ndiwo a mwa iwe, amene katundu wake anawakhalira mtonzo.
19 Taonani, nthawi yomweyo ndidzachita nao onse akuzunza iwe; ndipo ndidzapulumutsa wotsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopirikitsidwayo; ndipo ndidzawaika akhale chilemekezo ndi dzina, iwo amene manyazi ao anali m’dziko lonse.
20 Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ZEP/3-838b68b290a5f5d1b0ef62c8710cedad.mp3?version_id=1068—