Categories
MATEYU

MATEYU 3

Yohane Mbatizi

1 Ndipo masiku aja anadza Yohane Mbatizi, nalalikira m’chipululu cha Yudeya,

2 nanena, Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.

3 Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesayamneneri, kuti,

Mau a wofuula m’chipululu,

konzani khwalala la Ambuye,

lungamitsani njira zake.

4 Ndipo Yohane yekhayo anali nacho chovala chake cha ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m’chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wakuthengo.

5 Pamenepo panamtulukira iye a kuYerusalemu, ndi Yudeya yense, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordani;

6 nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordani, alikuwulula machimo ao.

7 Ndipo iye pakuona ambiri aAfarisindi aAsadukiakudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?

8 Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:

9 ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.

10 Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.

11 Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

12 chouluzira chake chili m’dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m’nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.

Abatizidwa Yesu

13 Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye.

14 Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?

15 Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.

16 Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;

17 ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/3-bc833b10ac131099146792f8c1078711.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *