Categories
MATEYU

MATEYU 11

Otumidwa ndi Yohane Mbatizi

1 Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozeraophunziraake khumi ndi awiri, Iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m’mizinda mwao.

2 Koma Yohane, pakumva m’nyumba yandende ntchito zaKhristu, anatumiza ophunzira ake mau,

3 nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?

4 Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona:

5 akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhateakonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.

6 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.

7 Ndipo m’mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

8 Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m’nyumba zamafumu.

9 Koma munatulukiranji? Kukaonamnenerikodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri.

10 Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti,

Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu,

amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu.

11 Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.

12 Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu.

13 Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chinanenera kufikira pa Yohane.

14 Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.

15 Amene ali ndi makutu akumva, amve.

16 Koma ndidzafanizira ndi chiyani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m’mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao.

17 Ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavine; tinabuma maliro, ndipo inu simunalire.

18 Pakuti Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi chiwanda.

19 Mwana wa Munthuanadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.

Mizinda itatu yosalapayo

20 Pomwepo Iye anayamba kutonza mizindayo, m’mene zinachitidwa zambiri za ntchito zamphamvu zake, chifukwa kuti siinatembenuke.

21 Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m’ziguduli ndi m’phulusa.

22 Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza mlandu wao wa Tiro ndi Sidoni udzachepa ndi wanu.

23 Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa mu Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.

24 Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa ndi wako.

Goli lake la Khristu

25 Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:

26 eetu, Atate, chifukwa chotero chinakhala chokondweretsa pamaso panu.

27 Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha, ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.

28 Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.

29 Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

30 Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/11-079470c932787ec5cd58e87de0a2d121.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *