Fanizo la antchito olembedwa mwinamwina
1 Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m’munda wake wampesa.
2 Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake.
3 Ndipo anatuluka dzuwa litakwera, naona ena ataima chabe pabwalo;
4 ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chili choyenera. Ndipo iwo anapita.
5 Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nachita chimodzimodzi.
6 Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe?
7 Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa.
8 Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba.
9 Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu aliyense rupiya latheka limodzi.
10 Ndipo m’mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka.
11 Koma m’mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja,
12 nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing’ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake.
13 Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangane ndi ine pa rupiya latheka limodzi?
14 Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe.
15 Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?
16 Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.
Funso la ana a Zebedeo
17 Ndipo pamene Yesu analikukwera kuYerusalemu, anatengaophunzirakhumi ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo,
18 Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipoMwana wa Munthuadzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa,
19 nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.
20 Pomwepo anadza kwa Iye amake a ana a Zebedeo ndi ana ake omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu.
21 Ndipo Iye anati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye ananena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu.
22 Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.
23 Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.
24 Ndipo m’mene khumiwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.
25 Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo.
26 Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;
27 ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:
28 monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.
Akhungu a ku Yeriko
29 Ndipo pamene iwo analikutuluka mu Yeriko, khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye.
30 Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m’mphepete mwa njira; m’mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anafuula nati, Mutichitire ife chifundo, Inu Mwana wa Davide.
31 Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide.
32 Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani?
33 Ananena kwa Iye, Ambuye, kuti maso athu apenye.
34 Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/20-f62cb8509cd814b40546f113af6fba13.mp3?version_id=1068—