Categories
YUDA

YUDA 1

1 Yuda, kapolo wa YesuKhristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu:

2 Chifundo ndi mtendere ndi chikondi zikuchulukireni.

Atsutsa aphunzitsi onyenga

3 Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.

4 Pakuti pali anthu ena anakwawira m’tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.

5 Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m’dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.

6 Angelonso amene sanasunge chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala paopao, adawasunga m’ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.

7 Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.

8 Momwemonso iwo m’kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero.

9 Koma Mikaele mkulu waangelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbike mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.

10 Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika.

11 Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m’njira ya Kaini, ndipo anadziononga m’chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m’chitsutsano cha Kora.

12 Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;

13 mafunde oopsa a nyanja, akuwinduka thovu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.

14 Ndipo kwa iwo, Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwaAdamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi,

15 kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zao zonse zosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.

16 Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.

17 Koma inu, abale, mukumbukire mau onenedwa kale ndiatumwia Ambuye wathu Yesu Khristu;

18 kuti ananena nanu, Pa nthawi yotsiriza padzakhala otonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo okha.

19 Iwo ndiwo opatukitsa, anthu a makhalidwe achibadwidwe, osakhala naye Mzimu.

Machenjezo; mayamiko kwa Mulungu

20 Koma inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera,

21 mudzisunge nokha m’chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kufikira moyo wosatha.

22 Ndipo ena osinkhasinkha muwachitire chifundo,

23 koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane naonso malaya ochitidwa mawanga ndi thupi.

24 Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m’kukondwera,

25 kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JUD/1-e46a32285ccc866be8bee9990b414ccb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *