Yesu achiritsa wa dzanja lopuwala
1 Ndipo analowanso m’sunagoge; ndipo munali munthu m’menemo ali ndi dzanja lake lopuwala.
2 Ndipo anamuyang’anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku laSabata; kuti ammange mlandu.
3 Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.
4 Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete.
5 Ndipo m’mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.
6 NdipoAfarisianatuluka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.
7 Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndiophunziraake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya,
8 ndi a kuYerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordani, ndi a kufupi ku Tiro ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo anazichita, linadza kwa Iye.
9 Ndipo anati kwa ophunzira ake, kuti kangalawa kamlinde Iye, chifukwa cha khamulo, kuti angamkanikize Iye,
10 pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze.
11 Ndipo mizimu yonyansa, m’mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.
12 Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye.
Apatula ophunzira khumi ndi awiri
13 Ndipo anakwera m’phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye.
14 Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira,
15 ndi kuti akhale nao ulamuliro wakutulutsa ziwanda.
16 Ndipo Simoni anamutcha Petro;
17 ndi Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo, iwo anawatcha Boaneje, ndiko kuti, Ana a bingu;
18 ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,
19 ndi Yudasi Iskariote, ndiye amene anampereka Iye.
Za Yesu ndi Belezebulu
Ndipo analowa m’nyumba.
20 Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya.
21 Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka.
22 Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali nayeBelezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.
23 Ndipo m’mene adawaitana iwo, ananena nao m’mafanizo,Satanaangathe bwanji kutulutsa Satana?
24 Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sungathe kukhazikika.
25 Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, singathe kukhazikika nyumbayo.
26 Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sangathe kukhazikika, koma atsirizika.
27 Komatu palibe munthu akhoza kulowa m’nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma ayambe wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m’nyumba mwake.
28 Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo;
29 koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha;
30 pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.
Abale ake a Yesu
31 Ndipo anadza amake ndi abale ake; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana.
32 Ndipo anthu ambiri anakhala pansi pomzinga; nanena kwa Iye, Onani, amanu ndi abale anu ali kunja akufunani Inu.
33 Ndipo anawayankha nanena, Amai wanga ndi abale anga ndani?
34 Ndipo anawaunguzaunguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga.
35 Pakuti aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/3-7c22451e30212b0d8e077d5bb546ab21.mp3?version_id=1068—