Categories
MARKO

MARKO 12

Fanizo la osungira munda

1 Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m’mafanizo. Munthu analima munda wampesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.

2 Ndipo m’nyengo yake anatuma kapolo kwa olimawo, kuti alandireko kwa olimawo zipatso za m’munda wampesa.

3 Ndipo iwo anamtenga iye, nampanda, namchotsa wopanda kanthu.

4 Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namchitira zomchititsa manyazi.

5 Ndipo anatuma wina; iyeyu anamupha; ndi ena ambiri; ena anawapanda, ndi ena anawapha.

6 Anamtsalira mmodzi, ndiye mwana wake wokondedwa; potsiriza anamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamchitira ulemu mwana wanga.

7 Koma olima ajawo, ananena mwa iwo okha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu.

8 Ndipo anamtenga, namupha iye, namtaya kunja kwa munda.

9 Pamenepo mwini munda adzachita chiyani? Adzafika, nadzaononga olimawo, nadzapereka mundawo kwa ena.

10 Kodi simunawerenge ngakhale lembo ili,

Mwala umene anaukana omanga nyumba,

womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:

11 Ichi chinachokera kwa Ambuye,

ndipo chili chozizwitsa m’maso mwathu?

12 Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka.

Za kupereka msonkho

13 Ndipo anatuma kwa Iye ena aAfarisindi a Aherode, kuti akamkole Iye m’kulankhula kwake.

14 Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang’ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwaKaisara, kapena iai?

15 Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa chinyengo chao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.

16 Ndipo ananena nao, Chithunzithunzi ichi, ndi chilembo chake zili za yani? Ndipo anati kwa Iye, Za Kaisara,

17 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri.

Asaduki afunsa za kuuka kwa akufa

18 Ndipo anadza kwa IyeAsaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye, nanena,

19 Mphunzitsi, Mose anatilembera, kuti, Akafa mbale wake wa munthu, nasiya mkazi, wosasiya mwana, mbale wake atenge mkazi wake, namuukitsire mbale wakeyo mbeu.

20 Analipo abale asanu ndi awiri; woyamba anakwatira mkazi, nafa, wosasiya mbeu;

21 ndipo wachiwiri anamkwatira, nafa, wosasiya mbeu; ndipo wachitatunso anatero momwemo;

22 ndipo asanu ndi awiriwo analibe kusiya mbeu. Potsiriza pake pa onse mkazinso anafa.

23 Pakuuka adzakhala mkazi wa yani wa iwowa? Pakuti asanu ndi awiriwo adamuyesa mkazi wao.

24 Yesu ananena nao, Simusochera nanga mwa ichi, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yake ya Mulungu?

25 Pakuti pamene adzauka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa; koma akhala ngatiangeloa Kumwamba. Koma za akufa, kuti akaukitsidwa;

26 simunawerenga m’buku la Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo?

27 Sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: musochera inu ndithu.

Lamulo loposa onse

28 Ndipo anadza mmodzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo pakudziwa kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Lamulo la m’tsogolo la onse ndi liti?

29 Yesu anayankha, kuti, La m’tsogolo ndili, Mvera, Israele; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi;

30 ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.

31 Lachiwiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.

32 Ndipo mlembiyo anati kwa Iye, Chabwino, Mphunzitsi, mwanena zoona kuti ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye:

33 ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzake monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.

34 Ndipo pakuona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kumfunsa Iye kanthu.

Khristu mwana wa Davide

35 Ndipo Yesu pamene anaphunzitsa mu Kachisi, anayankha, nanena, Bwanji alembi anena kutiKhristundiye mwana wa Davide?

36 Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.

37 Davide mwini yekha amtchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wake bwanji? Ndipo anthu a makamuwo anakondwa kumva Iye.

Yesu awachenjeza za Alembi

38 Ndipo m’chiphunzitso chake ananena, Yang’anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda ovala miinjiro, ndi kulonjeredwa pamisika,

39 ndi kukhala nayo mipando yaulemu m’sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando:

40 amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa.

Mphatso ya mkazi wamasiye

41 Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo ndalama, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni chuma ambiri anaponyamo zambiri.

42 Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tating’ono tokwanira kakobiri kamodzi.

43 Ndipo anaitanaophunziraake, nati kwa iwo, Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphawi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo:

44 pakuti anaponyamo onse mwa zochuluka zao; koma iye anaponya mwa kusowa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/12-49808ba024d1d004e935a63d8de06d00.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *