Maphedwe a Agalileya, nsanja ya Siloamu
1 Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasakaniza mwazi wao ndi nsembe zao.
2 Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akuchimwa koposa Agalileya onse, chifukwa anamva zowawa izi?
3 Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.
4 Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya mu Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m’Yerusalemu?
5 Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse chimodzimodzi.
Fanizo la mkuyu wosabala
6 Ndipo Iye ananenafanizoili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m’munda wake wampesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe.
7 Ndipo anati kwa wosungira munda wampesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake?
8 Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe;
9 ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.
Achiritsa mkazi wopeteka
10 Ndipo analikuphunzitsa m’sunagogemwina, tsiku laSabata.
11 Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.
12 Ndipo Yesu m’mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.
13 Ndipo anaika manja ake pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.
14 Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m’menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.
15 Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng’ombe yake, kapena bulu wake ku chodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi?
16 Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, ameneSatanaanammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata?
17 Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m’khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinachitidwa ndi Iye.
Fanizo la mpiru ndi la chotupitsa
18 Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani?
19 Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m’munda wakewake, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m’mlengalenga zinabindikira mu nthambi zake.
20 Ndiponso anati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi chiyani?
21 Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anatenga, nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupo wonsewo.
Khomo lopapatiza
22 Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu.
23 Ndipo munthu anati kwa Iye, Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo owerengeka kodi? Koma Iye anati kwa iwo,
24 Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.
25 Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako;
26 pomwepo mudzayamba kunena, Ife tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munaphunzitsa m’makwalala a kwathu;
27 ndipo Iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene muchokera inu; chokani pa Ine, nonse akuchita chosalungama.
28 Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mutulutsidwa kunja.
29 Ndipo anthu adzachokera kum’mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, nadzakhala pansi mu Ufumu wa Mulungu.
30 Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala oyamba, ndipo alipo oyamba adzakhala akuthungo.
Amchenjeza Yesu za Herode. Yesu alirira Yerusalemu
31 Nthawi yomweyo anadzapoAfarisiena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwaHerodeafuna kupha Inu.
32 Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.
33 Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi mkucha, chifukwa sikuloleka kutimneneriaonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu.
34 Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawirikawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m’mapiko ake, ndipo simunafunai!
35 Onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, Simudzandiona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka Iye amene akudza m’dzina la Ambuye.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/13-9528ed474be52e402ab33dfd17d49421.mp3?version_id=1068—