Categories
LUKA

LUKA 22

Yudasi apangana kupereka Yesu

1 Ndipo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa chinayandikira, ndicho chotchedwaPaska.

2 Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna maphedwe ake pakuti anaopa anthuwo.

3 NdipoSatanaanalowa mwa Yudasi wonenedwa Iskariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo.

4 Ndipo iye anachoka, nalankhulana ndi ansembe aakulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo.

5 Ndipo anakondwera, napangana naye kumpatsa ndalama.

6 Ndipo iye anavomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.

Paska lotsiriza. Mgonero

7 Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska.

8 Ndipo Iye anatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitani mutikonzere ife Paska, kuti tidye.

9 Ndipo iwo ananena naye, Mufuna tikakonzere kuti?

10 Ndipo Iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m’mzinda, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye.

11 Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chili kuti, m’mene ndikadye Paska pamodzi ndiophunziraanga?

12 Ndipo iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko.

13 Ndipo anapita iwo, napeza monga adatero nao; ndipo anakonza Paska.

14 Ndipo itadza nthawi yake, Iye anakhala pachakudya, ndi ophunzira pamodzi ndi Iye.

15 Ndipo anati kwa iwo, Ndinalakalaka ndithu kudya Paska uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa;

16 pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu.

17 Ndipo analandira chikho, ndipo pamene adayamika, anati, Landirani ichi, muchigawane mwa inu nokha;

18 pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika.

19 Ndipo m’mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.

20 Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.

21 Koma onani, dzanja lake la iye amene adzandipereka ali pagome pano pamodzi ndi Ine.

22 PakutiMwana wa Munthuamukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka!

23 Ndipo anayamba kufunsana mwa iwo okha, ndiye yani mwa iwo amene adzachita ichi.

Kutsutsana kwakuti wamkulu ndani?

24 Ndipo kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu.

25 Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, Ochitira zabwino.

26 Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng’ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.

27 Pakuti wamkulu ndani, iye wakuseama pachakudya kapena wakutumikirapo? Si ndiye wakuseama pachakudya kodi? Koma Ine ndili pakati pa inu monga ngati wotumikira.

28 Koma inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga;

29 ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga;

30 ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.

Yesu achenjeza Petro

31 Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;

32 koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.

33 Ndipo anati kwa Iye, Ambuye, ndilipo ndikapite ndi Inu kundende ndi kuimfa.

34 Ndipo Iye anati, Ndikuuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine.

35 Ndipo anati kwa iwo, Pamene ndinakutumizani opanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba, ndi nsapato, munasowa kanthu kodi? Anati iwo, Iai.

36 Ndipo anati kwa iwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga.

37 Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine zili nacho chimaliziro.

38 Ndipo iwo anati, Ambuye, taonani, malupanga awiri siwa. Ndipo anati kwa iwo, Chakwanira.

Yesu mu Getsemani

39 Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye.

40 Ndipo pofika pomwepo, anati kwa iwo, Pempherani kuti mungalowe m’kuyesedwa.

41 Ndipo anapatukana nao kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera,

42 nati, Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kuchitike.

43 Ndipo anamuonekera Iyemngelowa Kumwamba namlimbitsa Iye.

44 Ndipo pokhala Iye m’chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.

45 Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m’tulo ndi chisoni,

46 ndipo anati kwa iwo, Mugoneranji? Ukani, pempherani kuti mungalowe m’kuyesedwa.

Amgwira Yesu

47 Pamene Iye anali chilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona Iye.

48 Koma Yesu anati kwa iye, Yudasi, ulikupereka Mwana wa Munthu ndi chimpsompsono kodi?

49 Ndipo m’mene iwo akumzinga Iye anaona chimene chiti chichitike, anati, Ambuye, tidzakantha ndi lupanga kodi?

50 Ndipo wina wa iwo anakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake lamanja.

51 Koma Yesu anayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo anakhudza khutu lake, namchiritsa.

52 Ndipo Yesu anati kwa ansembe aakulu ndi akapitao a Kachisi, ndi akulu, amene anadza kumgwira Iye, Munatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wachifwamba?

53 Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.

Petro akana Yesu

54 Ndipo pamenepo anamgwira Iye, napita naye, nalowa m’nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutali.

55 Ndipo pamene adasonkha moto m’kati mwa bwalo, nakhala pansi pamodzi, Petro anakhala pakati pao.

56 Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m’kuwala kwake kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye.

57 Koma anakana, nati, Mkaziwe, sindimdziwa Iye.

58 Ndipo popita kamphindi, anamuona wina, nati, Iwenso uli mmodzi wa awo. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindine.

59 Ndipo patapita ngati ora limodzi, wina ananenetsa, kuti, Zoonadi, munthu uyunso anali naye, pakuti ndiye Mgalileya

60 Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa chimene uchinena. Ndipo pomwepo, iye ali chilankhulire, tambala analira.

61 Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang’ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.

62 Ndipo anatuluka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.

Yesu pa bwalo la akulu a Ayuda

63 Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza Iye, nampanda.

64 Ndipo anamkulunga Iye m’maso, namfunsa, nati, Talota; anakupanda Iwe ndani?

65 Ndipo zambiri zina anamnenera Iye, namchitira mwano.

66 Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao,

67 nanena, Ngati uliKhristu, utiuze. Ndipo anati kwa iwo, Ndikakuuzani, simudzavomereza;

68 ndipo ndikakufunsani kanthu, simudzayankha.

69 Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthu adzakhala padzanja lamanja la mphamvu ya Mulungu.

70 Ndipo onse anati, Umo mtero, muli Mwana wa Mulungu kodi? Ndipo Iye anati kwa iwo, Munena kuti ndine.

71 Ndipo iwo anati, Tifuniranjinso mboni? Pakuti ife tokha tinamva m’kamwa mwa Iye mwini.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/22-254cf6b52b058c7d14ee93ce15c297bd.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *