Yesu auka kwa akufa
1 Koma tsiku loyamba la sabata, mbandakucha, anadza kumanda atatenga zonunkhira adazikonza.
2 Ndipo anapeza mwala unakunkhunizidwa kuuchotsa pamanda.
3 Ndipo m’mene analowa sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu.
4 Ndipo kunali, m’mene anathedwa nzeru nacho, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atavala zonyezimira;
5 ndipo m’mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?
6 Palibe kuno Iye, komatu anauka; kumbukirani muja adalankhula nanu, pamene analinso mu Galileya,
7 ndi kunena, kuti,Mwana wa Munthuayenera kuperekedwa m’manja a anthu ochimwa, ndi kupachikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lachitatu.
8 Ndipo anakumbukira mau ake,
9 nabwera kuchokera kumanda, nafotokozera zonse khumi ndi mmodziwo, ndi otsala onse omwe.
10 Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwaatumwiwo.
11 Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zachabe, ndipo sanamvere akaziwo.
12 Koma Petro ananyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama anaona nsalu zabafuta pazokha; ndipo anachoka nanka kwao, nazizwa ndi chija chidachitikacho.
Zochitika panjira ya ku Emausi
13 Ndipo taonani, awiri a mwa iwo analikupita tsiku lomwelo kumudzi dzina lake Emausi, wosiyana ndiYerusalemumastadiya makumi asanu ndi limodzi.
14 Ndipo iwowa anakambirana nkhani za izi zonse zidachitika.
15 Ndipo kunali m’kukambirana kwao ndi kufunsana, Yesu mwini anayandikira, natsagana nao.
16 Koma maso ao anagwidwa kuti asamzindikire Iye.
17 Ndipo anati kwa iwo, Mau awa ndi otani mulandizanawo poyendayenda? Ndipo anaima ndi nkhope zao zachisoni.
18 Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lake Kleopa, anayankha nati kwa Iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo mu Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano?
19 Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarene, ndiye munthumneneriwamphamvu m’ntchito, ndi m’mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;
20 ndi kuti ansembe aakulu ndi akulu athu anampereka Iye ku chiweruziro cha imfa, nampachika Iye pamtanda.
21 Ndipo tinayembekeza ife kuti Iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israele. Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lachitatu kuyambira zidachitika izi.
22 Komatu akazi enanso a mwa ife anatidabwitsa, ndiwo amene analawirira kumanda;
23 ndipo m’mene sanapeze mtembo wake, anadza, nanena kuti adaona m’masomphenyaangelo, amene ananena kuti ali ndi moyo Iye.
24 Ndipo ena a iwo anali nafe anachoka kunka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sanamuone.
25 Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!
26 Kodi sanayenereKhristukumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake?
27 Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m’malembo onse zinthu za Iye yekha.
28 Ndipo anayandikira kumudzi umene analikupitako; ndipo anachita ngati anafuna kupitirira.
29 Ndipo anamuumiriza Iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo analowa kukhala nao.
30 Ndipo kunali m’mene Iye anaseama nao pachakudya, anatenga mkate, naudalitsa, naunyema, napatsa iwo.
31 Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira Iye; ndipo anawakanganukira Iye, nawachokera.
32 Ndipo anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m’kati mwathu nanga m’mene analankhula nafe m’njira, m’mene anatitsegulira malembo?
33 Ndipo ananyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi mmodziwo, ndi iwo anali nao atasonkhana pamodzi,
34 nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni.
35 Ndipo iwo anawafotokozera za m’njira, ndi umo anadziwika nao m’kunyema kwa mkate.
Yesu aonekera kwa khumi ndi mmodziwo
36 Ndipo pakulankhula izi iwowa, Iye anaimirira pakati pao; nanena nao, Mtendere ukhale nanu.
37 Koma anaopsedwa ndi kuchita mantha, nayesa alikuona mzimu.
38 Ndipo anati kwa iwo, Mukhala bwanji ovutika? Ndipo matsutsano amauka bwanji m’mtima mwanu?
39 Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti Ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muona ndili nazo Ine.
40 Ndipo m’mene ananena ichi, anawaonetsera iwo manja ake ndi mapazi ake.
41 Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno?
42 Ndipo anampatsa Iye chidutsu cha nsomba yokazinga.
43 Ndipo anachitenga, nachidya pamaso pao.
44 Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m’chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.
45 Ndipo anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo;
46 ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;
47 ndi kuti kulalikidwe m’dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.
48 Inu ndinu mboni za izi.
49 Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m’mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.
Yesu akwera kunka Kumwamba
50 Ndipo anatuluka nao kufikira ku Betaniya; nakweza manja ake, nawadalitsa.
51 Ndipo kunali, pakuwadalitsa Iye analekana nao, natengedwa kunka Kumwamba.
52 Ndipo anamlambira Iye, nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu;
53 ndipo anakhala chikhalire mu Kachisi, nalikuyamika Mulungu.Amen.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/24-63d52fda51d2c9ca46d8a7457ea112f5.mp3?version_id=1068—