Abale a Yesu samvomereza
1 Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.
2 Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira.
3 Chifukwa chake abale ake anati kwa Iye, Chokani pano, mumuke ku Yudeya, kutiophunziraanunso akapenye ntchito zanu zimene muchita.
4 Pakuti palibe munthu achita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera. Ngati muchita izi, dzionetsereni eni nokha kwa dziko lapansi.
5 Pakuti angakhale abale ake sanakhulupirire Iye.
6 Chifukwa chake Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse.
7 Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.
8 Kwerani inu kunka kuphwando; sindikwera Ine kuphwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire.
9 Ndipo m’mene adanena nao zimenezi anakhalabe mu Galileya.
Yesu aphunzitsa mu Kachisi. Ayesa kumgwira
10 Koma pamene abale ake adakwera kunka kuchikondwerero, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika.
11 Pomwepo Ayuda analikumfuna Iye pachikondwerero, nanena, Ali kuti uja?
12 Ndipo kunali kung’ung’udza kwambiri za Iye m’makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo.
13 Chinkana anatero panalibe munthu analankhula za Iye poyera, chifukwa cha kuopa Ayuda.
14 Koma pamene padafika pakati pa chikondwerero, Yesu anakwera nalowa mu Kachisi, naphunzitsa.
15 Chifukwa chake Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?
16 Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.
17 Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.
18 Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.
19 Si Mose kodi anakupatsani inu chilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu achita chilamulo? Mufuna kundipha chifukwa ninji?
20 Khamu la anthu linayankha, Muli ndi chiwanda: afuna ndani kukuphani Inu?
21 Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinachita ntchito imodzi, ndipo muzizwa monse.
22 Chifukwa cha ichi Mose anakupatsani inumdulidwe(si kuti uchokera kwa Mose, koma kwa makolo); ndipo mudula munthu tsiku laSabata.
23 Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata?
24 Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.
25 Pamenepo ena a iwo a kuYerusalemuananena, Kodi suyu amene afuna kumupha?
26 Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiyeKhristuameneyo?
27 Koma ameneyo tidziwa uko achokera: koma Khristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko achokera.
28 Pamenepo Yesu anafuula mu Kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndichokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.
29 Ine ndimdziwa Iye; chifukwa ndili wochokera kwa Iye, nandituma Ine Iyeyu.
30 Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.
31 Koma ambiri a m’khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?
32 Afarisianamva khamu la anthu ling’ung’udza zimenezi za Iye; ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire Iye.
33 Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndili ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine.
34 Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo.
35 Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki?
36 Mau awa amene ananena ndi chiyani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine: ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo?
Yesu aneneratu za Mzimu Woyera
37 Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.
38 Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m’kati mwake.
39 Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.
Anthu atsutsana za Iye
40 Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena,Mneneriyo ndi uyu ndithu.
41 Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka mu Galileya?
42 Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?
43 Kudakhala tsono kusiyana m’khamulo chifukwa cha Iye.
44 Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja.
45 Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe aakulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenge Iye bwanji?
46 Anyamatawo anayankha, Nthawi yonse palibe munthu analankhula chotero.
47 Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso?
48 Kodi wina wa akulu anakhulupirira Iye, kapena wa Afarisi?
49 Koma khamu ili losadziwa chilamulo, likhala lotembereredwa.
50 Nikodemo ananena kwa iwo, amene uja adadza kwa Iye kale, ali mmodzi wa iwo,
51 Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?
52 Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya? Santhula, nuone kuti mu Galileya sanauke mneneri.
53 Ndipo anamuka munthu yense kunyumba yake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JHN/7-5b1c141fa61ac62554bd106b19a72f85.mp3?version_id=1068—