Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 17

Paulo ku Tesalonika ndi Berea

1 Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunalisunagogewa Ayuda.

2 Ndipo Paulo, monga amachita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m’malembo, natanthauzira,

3 natsimikiza, kuti kunayeneraKhristukumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.

4 Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Silasi; ndi Agriki akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi aakulu osati owerengeka.

5 Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m’mzinda; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu.

6 Pamene sanawapeze anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akulu a mzinda, nafuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;

7 amene Yasoni walandira; ndipo onsewo achita zokana malamulo aKaisara; nanena kuti pali mfumu ina, Yesu.

8 Ndipo anavuta anthu, ndi akulu a mzinda, pamene anamva zimenezi.

9 Ndipo pamene analandira chikole kwa Yasoni ndi enawo, anawamasula.

10 Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Silasi usiku kunka ku Berea; pamene iwo anafika komweko analowa m’sunagoge wa Ayuda.

11 Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.

12 Ndipo ambiri a iwo anakhulupirira; ndi akazi a Chigriki omveka, ndi amuna, osati owerengeka.

13 Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereanso, anadza komwekonso, nautsa, navuta makamu.

14 Pomwepo abale anatulutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Silasi ndi Timoteo anakhalabe komweko.

Paulo ku Atene

15 Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Silasi ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu chonse, anachoka.

16 Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mzinda wonse wadzala ndi mafano.

17 Chotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m’sunagoge, ndi m’bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.

18 Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.

19 Ndipo anamgwira, nanka naye kuAreopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa chiphunzitso ichi chatsopano uchinena iwe?

20 Pakuti ufika nazo kumakutu athu zachilendo: tifuna tsono kudziwa, izi zitani?

21 (Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva cha tsopano.)

22 Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati, Amuna inu a Atene, m’zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.

23 Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.

24 Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo ndiye Ambuye, mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja;

25 satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;

26 ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;

27 kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife;

28 pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuimba anu ati, Pakuti ifenso tili mbadwa zake.

29 Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapenasiliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.

30 Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima;

31 chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.

32 Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.

33 Choncho Paulo anatuluka pakati pao.

34 Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupirira; mwa iwonso munali Dionizio Mwareopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/17-466a46e1480558cd878479aeeea7f039.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *