Paulo atabwera ku Yerusalemu amgwira mu Kachisi
1 Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Kosi, ndi m’mawa mwake ku Rode, ndipo pochokerapo ku Patara;
2 ndipo m’mene tinapeza ngalawa yakuoloka kunka ku Fenisiya, tinalowamo, ndi kupita nayo.
3 Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kipro, tinachisiya kulamanzere, nkupita ku Siriya; ndipo tinakocheza ku Tiro; pakuti pamenepo ngalawa inafuna kutula akatundu ake.
4 Ndipo m’mene tinapezaophunzira, tinakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere kuYerusalemu.
5 Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m’mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,
6 ndi kulawirana; ndipo tinalowa m’ngalawa, koma iwo anabwera kwao.
7 Ndipo ife titatsiriza ulendo wathu wochokera ku Tiro, tinafika ku Ptolemaisi; ndipo m’mene tidalonjera abale, tinakhala nao tsiku limodzi.
8 Ndipo m’mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m’mene tinalowa m’nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.
9 Ndipo munthuyu anali nao ana aakazi anai, anamwali, amene ananenera.
10 Ndipo pokhalapo masiku ambiri, anatsika ku Yudeyamneneri, dzina lake Agabu.
11 Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a mu Yerusalemu, nadzampereka m’manja aamitundu.
12 Koma pamene tinamva izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko, asakwere iye kunka ku Yerusalemu.
13 Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.
14 Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kuchitidwe.
15 Ndipo atapita masiku awa tinakonza akatundu athu, ntikwera ku Yerusalemu.
16 Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.
17 Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale anatilandira mokondwera.
18 Ndipo m’mawa mwake Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo.
19 Ndipo atawalonjera iwo, anawafotokozera chimodzichimodzi zimene Mulungu anachita kwa amitundu mwa utumiki wake.
20 Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;
21 ndipo anamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana ao, kapena asayende monga mwa miyambo.
22 Nchiyani tsono? Adzamva ndithu kuti wafika.
23 Chifukwa chake uchite ichi tikuuza iwe; tili nao amuna anai amene anawinda;
24 amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo.
25 Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.
26 Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m’mawa mwake m’mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa mu Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.
27 Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye mu Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,
28 nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao mu Kachisi, nadetsa malo ano oyera.
29 Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye ku Kachisi.
30 Ndipo mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa mu Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.
31 Ndipo m’mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkulu wa gululo kuti mu Yerusalemu monse muli piringupiringu.
32 Ndipo posachedwa iye anatenga asilikali ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkulu ndi asilikali, analeka kumpanda Paulo.
33 Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani?
34 Koma wina anafuula kena, wina kena, m’khamumo; ndipo m’mene sanathe kudziwa zoona chifukwa cha phokosolo analamulira amuke naye kulinga.
35 Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikali chifukwa cha kulimbalimba kwa khamulo;
36 pakuti unyinji wa anthu unatsata, nufuula, Mchotse iye.
37 Ndipo poti alowe naye m’linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki?
38 Si ndiwe Mwejipito uja kodi, unachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kuchipululu?
39 Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa mu Silisiya, mfulu ya mzinda womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu.
40 Ndipo m’mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m’chinenedwe cha Chihebri, nanena:
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/21-511529252834baaf16f306f15a2d6882.mp3?version_id=1068—