Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 24

Felikisi amva mlandu wa Paulo

1 Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.

2 Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,

3 tizilandira ndi chiyamiko chonse, monsemo ndi ponsepo, Felikisi womveka inu.

4 Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu.

5 Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m’dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;

6 amenenso anayesa kuipsa Kachisi; amene tamgwira.

8 Ndipo kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za izi zonse timnenerazi.

9 Ndipo Ayudanso anavomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero.

10 Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;

11 popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha chikwerere ine kuYerusalemukukalambira;

12 ndipo sanandipeze mu Kachisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m’sunagogekapena m’mzinda.

13 Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano.

14 Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;

15 ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo okhanso achilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.

16 M’menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.

17 Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;

18 popereka izi anandipeza woyeretsedwa mu Kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso;

19 koma panali Ayuda ena a ku Asiya, ndiwo mwenzi atakhala pano pamaso panu ndi kundinenera, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine.

20 Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza chosalungama chotani, poimirira ine pamaso pabwalo la akulu a milandu,

21 koma mau awa amodzi okha, amene ndinafuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.

22 Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.

23 Ndipo analamulirakenturiyoamsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira.

24 Koma atapita masiku ena, anadza Felikisi ndi Durusila mkazi wake, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za chikhulupiriro chaKhristuYesu.

25 Ndipo m’mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.

26 Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; chifukwa chakenso anamuitana iye kawirikawiri, nakamba naye.

27 Koma zitapita zaka ziwiri Porkio Fesito analowa m’malo a Felikisi; ndipo Felikisi pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m’nsinga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/24-10fce9817b34fbdfb4df072bb1525c7f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *