Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 8

Atsegula chosindikiza chachisanu ndi chiwiri. Angelo asanu ndi awiri, ndi malipenga oyamba anai

1 Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chiwiri, munali chete mu Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.

2 Ndipo ndinaonaangeloasanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.

3 Ndipo anadza mngelo wina, naima paguwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse paguwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.

4 Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m’dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.

5 Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala paguwa la nsembe, nauponya padziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi.

6 Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe.

7 Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosakaniza ndi mwazi, ndipo anazitaya padziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.

8 Ndipo mngelo wachiwiri anaomba lipenga, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto linaponyedwa m’nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi;

9 ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa zili m’nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka.

10 Ndipo mngelo wachitatu anaomba lipenga, ndipo idagwa kuchokera kumwamba nyenyezi yaikulu, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi;

11 ndipo dzina lake la nyenyeziwo alitcha Chowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti asananduka owawa.

12 Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.

13 Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pamwamba, ndi kunena ndi mau aakulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/8-9189d1753cce6e725ef86f55970fabbb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *