Amtumiza Paulo ku Roma. Tsoka panyanja
1 Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m’ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwakenturiyodzina lake Julio, wa gulu la Augusto.
2 Ndipo m’mene tidalowa m’ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.
3 Ndipo m’mawa mwake tinangokocheza ku Sidoni; ndipo Julio anachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze.
4 Ndipo pokankhanso pamenepo, tinapita kuseri kwa Kipro, popeza mphepo inaomba mokomana nafe.
5 Ndipo pamene tidapyola nyanja ya kunsi kwake kwa Silisiya ndi Pamfiliya, tinafika ku Mira wa Likiya.
6 Ndipo kenturiyo anapezako ngalawa ya ku Aleksandriya, ilikupita ku Italiya, ndipo anatilongamo.
7 Ndipo m’mene tidapita pang’onopang’ono masiku ambiri, ndi kufika movutika pandunji pa Kinido, ndipo popeza siinatilolanso mphepo, tinapita m’tseri mwa Krete, pandunji pa Salimone;
8 ndipo popazapazapo movutika, tinafika kumalo ena dzina lake Pokocheza Pokoma; pafupi pamenepo panali mzinda wa Lasea.
9 Ndipo itapita nthawi yambiri, ndipo unayambokhala woopsa ulendowo, popezanso nyengo ya kusala chakudya idapita kale, Paulo anawachenjeza,
10 nanena nao, Amuna inu, ndiona ine kuti ulendo udzatitengera kuonongeka ndi kutayika kwambiri, si kwa akatundu okha kapena ngalawa yokha, komatunso kwa moyo wathu.
11 Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo.
12 Ndipo popeza dooko silinakome kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera.
13 Ndipo poomba pang’ono mwera, poyesa kuti anaona chofunirako, anakoka nangula, napita m’mbali mwa Krete.
14 Koma patapita pang’ono idaombetsa kuchokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Yurakulo;
15 ndipo pogwidwa nayo ngalawa, yosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tinangotengedwa.
16 Ndipo popita kuseri kwa chisumbu chaching’ono dzina lake Kauda, tinakhoza kumangitsa bwato koma movutika;
17 ndipo m’mene adaukweza, anachita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Siriti, anatsitsa matanga, natengedwa motero.
18 Ndipo povutika kwakukulu ndi namondweyo, m’mawa mwake anayamba kutaya akatundu;
19 ndipo tsiku lachitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa.
20 Ndipo m’mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalire masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng’ono anatigwera, chiyembekezo chonse chakuti tipulumuke chidatichokera pomwepo.
21 Ndipo pamene atakhala nthawi yaikulu osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.
22 Koma tsopano ndikuchenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo.
23 Pakuti anaimirira kwa ine usiku waleromngelowa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira,
24 nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso paKaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.
25 Chifukwa chake, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine.
26 Koma tiyenera kutayika pa chisumbu chakuti.
27 Koma pofika usiku wakhumi ndi chinai, potengedwa ife kwina ndi kwina m’nyanja ya Adriya, pakati pa usiku amalinyero anazindikira kuti analikuyandikira kumtunda;
28 ndipo anayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri; ndipo katapita kanthawi, anayesanso, napeza mikwamba khumi ndi isanu.
29 Ndipo pakuopa tingatayike pamiyala, anaponya anangula anai kumakaliro, nakhumba kuti kuche.
30 Ndipo m’mene amalinyero anafuna kuthawa m’ngalawa, natsitsira bwato m’nyanja, monga ngati anati aponye anangula kulikulu,
31 Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikali, Ngati awa sakhala m’ngalawa inu simukhoza kupulumuka.
32 Pamenepo asilikali anadula zingwe za bwato, naligwetsa.
33 Ndipo popeza kulinkucha, Paulo anawachenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi chinai limene munalindira, ndi kusala chakudya, osalawa kanthu.
34 Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pamutu wa mmodzi wa inu.
35 Ndipo atanena izi, ndi kutenga mkate, anayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m’mene adaunyema anayamba kudya.
36 Ndipo anakhala olimbika mtima onse, natenga chakudya iwo omwe.
37 Ndipo ife tonse tili m’ngalawa ndife anthu mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi mmodzi.
38 Ndipo m’mene anakhuta, anapepuza ngalawa, nataya tirigu m’nyanja.
39 Ndipo kutacha sanazindikire dzikolo; koma anaona pali bondo la mchenga; kumeneko anafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako ngalawa.
40 Ndipo m’mene anataya anangula anawasiya m’nyanja, namasulanso zingwe zomanga tsigiro; ndipo pokweza thanga la kulikulu, analunjikitsa kumchenga.
41 Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikulu kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde.
42 Ndipo uphungu wa asilikali udati awaphe andende, angasambire, ndi kuthawa.
43 Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angachite cha uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m’nyanja, nafike pamtunda,
44 ndipo otsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa zina za m’ngalawa. Ndipo kudatero kuti onse adapulumukira pamtunda.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/27-64a25c3e84ce4b1a1a497f8d1fd31670.mp3?version_id=1068—