Kusamvera kwa Ayuda
1 Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m’mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.
2 Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akuchita zotere.
3 Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wa Mulungu?
4 Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?
5 Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;
6 amene adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake;
7 kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;
8 koma kwa iwo andeu, ndi osamvera choonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza,
9 nsautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu aliyense wakuchita zoipa, kuyambira Myuda, komanso Mgriki;
10 koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki;
11 pakuti Mulungu alibe tsankho.
12 Pakuti onse amene anachimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo;
13 pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama.
14 Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo;
15 popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m’mitima yao, ndipo chikumbumtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana;
16 tsiku limene Mulungu adzaweruza ndiKhristuYesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.
Ayuda atsutsidwa
17 Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu,
18 nudziwa chifuniro chake, nuvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m’chilamulo,
19 nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima,
20 wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m’chilamulo ndi chionekedwe cha nzeru ndi cha choonadi;
21 ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?
22 Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za mu Kachisi kodi?
23 Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m’chilamulo?
24 Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.
Mdulidwe woona
25 Pakuti indemdulidweuli wabwino, ngati iwe umachita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa.
26 Chifukwa chake ngati wosadulidwa asunga zoikika za chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikudzayesedwa ngati mdulidwe?
27 Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo?
28 Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupimo;
29 koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m’malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/2-20bf2115e952ec289bbd0355776589b8.mp3?version_id=1068—