Categories
AROMA

AROMA 11

Mulungu sanataye Aisraele onse

1 Chifukwa chake ndinena, Mulungu anataya anthu ake kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndili Mwisraele, wa mbeu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini.

2 Mulungu sanataye anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kapena simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Kuti anaumirira Mulungu poneneza Israele, kuti,

3 Ambuye, anawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndipo ine ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga.

4 Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu aamuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadireBaala.

5 Choteronso nthawi yatsopano chilipo chotsalira monga mwa kusankha kwa chisomo.

6 Koma ngati kuli ndi chisomo, sikulinso ndi ntchito ai; ndipo pakapanda kutero, chisomo sichikhalanso chisomo.

7 Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israele afunafuna sanachipeze; koma osankhidwawo anachipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;

8 monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.

9 Ndipo Davide akuti,

Gome lao likhale kwa iwo, ngati msampha, ndi ngati diwa,

ndi monga chokhumudwitsa, ndi chowabwezera chilango;

10 maso ao adetsedwe, kuti asapenye,

ndipo muweramitse msana wao masiku onse.

11 Chifukwa chake ndinena, Anakhumudwa kodi kuti agwe? Msatero ai; koma ndi kulakwa kwao chipulumutso chinadza kwa anthu akunja, kudzachititsa iwo nsanje.

12 Ndipo ngati kulakwa kwao, kwatengera dziko lapansi zolemera, ndipo kuchepa kwao kutengera anthuamitunduzolemera; koposa kotani nanga kudzaza kwao?

Potsiriza Mulungu adzapulumutsa Israele

13 Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndilimtumwiwa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga;

14 kuti ngati nkutheka ndikachititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo.

15 Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuyanjanitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakuchokera kwa akufa?

16 Ndipo ngati zipatso zoyamba zili zopatulika, choteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, choteronso nthambi.

17 Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wakuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo,

18 usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu.

19 Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikalumikizidwe nao.

20 Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:

21 pakuti ngati Mulungu sanaleke nthambi za mtundu wake, inde sadzakuleka iwe.

22 Chifukwa chake onani kukoma mtima ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwake; koma kwa iwe kukoma mtima kwake kwa Mulungu, ngati ukhala chikhalire m’kukoma mtimamo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.

23 Ndipo iwonso, ngati sakhala chikhalire mu kusakhulupirira, adzawalumikizanso, pakuti Mulungu ali wamphamvu yakutha kuwalumikizanso.

24 Pakuti ngati iwe unasadzidwa kumtengo waazitonawa mtundu wakuthengo, ndipo unalumikizidwa ndi mtengo wa azitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wake, adzalumikizidwa ndi mtengo wao womwewo wa azitona?

25 Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang’ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;

26 ndipo chotero Israele yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti,

Adzatuluka kuZiyoniMpulumutsi;

Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo:

27 Ndipo ichi ndichipanganochanga ndi iwo,

pamene ndidzachotsa machimo ao.

28 Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, chifukwa cha inu; koma kunena za chisankhidwe, ali okondedwa, chifukwa cha makolo.

29 Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika.

30 Pakuti monga inunso kale simunamvere Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo mwa kusamvera kwao,

31 choteronso iwo sanamvere tsopano, kuti iwonso akalandire chifundo, chifukwa cha chifundo cha kwa inu.

32 Pakuti Mulungu anatsekera pamodzi onse m’kusamvera, kuti akachitire onse chifundo.

Ulemu waukulu wa Mulungu

33 Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!

34 Pakuti anadziwitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala phungu wake ndani?

35 Ndipo anayamba ndani kumpatsa Iye, ndipo adzambwezeranso?

36 Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/11-0366ed0e0c9b4e03dada5fbc2df45978.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *