Kugonjera kwathu kwa akulu
1 Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.
2 Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.
3 Pakuti mafumu sakhala oopsa ntchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m’menemo:
4 pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.
5 Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima.
6 Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi.
7 Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.
Kukondana, kudikira, chiyero
8 Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.
9 Pakuti ili, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina lililonse, limangika pamodzi m’mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.
10 Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chili chokwanitsa lamulo.
11 Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira.
12 Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika.
13 Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m’madyerero ndi kuledzera ai, si m’chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.
14 Koma valani inu Ambuye YesuKhristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/13-cb7d964499b126a885a96adc26075530.mp3?version_id=1068—