Categories
1 AKORINTO

1 AKORINTO 4

Atumiki a Khristu ndi ogawira zinsinsi za Mulungu

1 Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki aKhristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.

2 Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.

3 Koma kwa ine kuli kanthu kakang’ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.

4 Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m’menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.

5 Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Kudzikuza kwa Akorinto, kudzichepetsa kwa Atumwi

6 Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.

7 Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?

8 Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.

9 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ifeatumwiotsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwaangelo, ndi kwa anthu.

10 Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.

11 Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika;

12 ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;

13 ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano.

14 Sindilembera izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga okondedwa.

15 Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwaKhristuYesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.

16 Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine.

17 Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo muMipingoyonse.

18 Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.

19 Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.

20 Pakuti ufumu wa Mulungu suli m’mau, koma mumphamvu. Mufuna chiyani?

21 Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/4-96c635c252617c83e02222b74e6da626.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *