Mbumba ya Seti
1 Ili ndi buku la mibadwo yaAdamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m’chifanizo cha Mulungu;
2 anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo natcha mtundu wao anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo.
3 Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m’chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.
4 Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.
5 Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.
6 Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi;
7 ndipo Seti anakhala ndi moyo, atabala Enosi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza zisanu ndi ziwiri: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi:
8 masiku ake onse a Seti anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi ndi ziwiri; ndipo anamwalira.
9 Ndipo Enosi anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi anai, nabala Kenani;
10 ndipo anakhala ndi moyo Enosi, atabala Kenani, zaka mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi zisanu: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.
11 Masiku ake onse a Enosi anali mazana asanu ndi anai kudza zisanu; ndipo anamwalira.
12 Ndipo Kenani anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, ndipo anabala Mahalalele:
13 ndipo Kenani anakhala ndi moyo, atabala Mahalalele zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi anai, ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi;
14 masiku ake onse a Kenani anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi; ndipo anamwalira.
15 Ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Yaredi;
16 ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo, atabala Yaredi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi:
17 masiku ake onse a Mahalalele anali zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu; ndipo anamwalira.
18 Ndipo Yaredi anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri, nabala Enoki;
19 ndipo Yaredi anakhala ndi moyo, atabala Enoki, zaka mazana asanu ndi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;
20 masiku ake onse a Yaredi anali zaka mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri: ndipo anamwalira.
21 Ndipo Enoki anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela:
22 ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;
23 masiku ake onse a Enoki anali mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu;
24 ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga.
25 Ndipo Metusela anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi ziwiri, nabala Lameki;
26 ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameki, zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala ana aamuna ndi aakazi:
27 masiku ake onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira.
28 Ndipo Lameki anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala mwana wamwamuna;
29 namutcha dzina lake Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pantchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova;
30 ndipo Lameki anakhala ndi moyo atabala Nowa, zaka mazana asanu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu, nabala ana aamuna ndi aakazi:
31 masiku ake onse a Lameki anali zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamwalira.
32 Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/5-5497e13ae5cfc699d1f1fe13e0e05f3f.mp3?version_id=1068—