Categories
GENESIS

GENESIS 30

1 Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.

2 Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m’malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba?

3 Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.

4 Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wake akhale mkazi wake; ndipo Yakobo analowa kwa iye.

5 Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna.

6 Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani.

7 Ndipo Biliha mdzakazi wake wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri.

8 Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamutcha dzina lake Nafutali.

9 Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.

10 Ndipo Zilipa mdzakazi wake wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna.

11 Ndipo Leya anati, Wamwai ine! Ndipo anamutcha dzina lake Gadi.

12 Ndipo Zilipa mdzakazi wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri.

13 Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana aakazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere.

14 Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m’thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.

15 Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.

16 Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo.

17 Ndipo Mulungu anamvera Leya, ndipo anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu.

18 Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara.

19 Ndipo Leya anatenganso pakati nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi.

20 Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana aamuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni.

21 Pambuyo pake ndipo anabala mwana wamkazi, namutcha dzina lake Dina.

22 Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m’mimba mwake.

23 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wachotsa manyazi anga;

24 namutcha dzina lake Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina.

Labani apangana ndi Yakobo

25 Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa.

26 Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.

27 Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, chifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine chifukwa cha iwe.

28 Ndipo iye anati, Undipangire ine malipiro ako, ndipo ndidzakupatsa.

29 Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe chomwe ndakutumikira iwe ndi chomwe zachita zoweta zako ndi ine.

30 Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kulikonse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa?

31 Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandichitira ine chotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako.

32 Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse kusankhasankha m’menemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamawangamawanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamawangamawanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.

33 Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m’tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.

34 Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako.

35 Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde amene anali amipyololomipyololo ndi amathothomathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamawangamawanga ndi zamathothomathotho zonse zinali zoyera pang’ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m’dzanja la ana ake aamuna.

36 Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani.

37 Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wauwisi wa libne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m’menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m’nthyolemo.

38 Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m’michera yakumwera, m’mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.

39 Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathothomathotho, ndi zamawangamawanga.

40 Ndipo Yakobo analekanitsa anaankhosa naziika pa zoweta za kuti ziyang’anire zamipyololomipyololo, ndi zakuda zonse za m’zoweta za Labani.

41 Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m’micheramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo.

42 Koma pamene ziweto zinali zofooka, sanaziike zimenezo: ndipo zofooka, zinali za Labani, ndi zolimba zinali za Yakobo.

43 Munthuyo ndipo analemera kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo aamuna ndi aakazi, ndingamira, ndi abulu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/30-e6e40d35f373542b400321411c9183aa.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *