Yakobo afuna kwao nathawa nazo zake
1 Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m’zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse.
2 Ndipo Yakobo anaona nkhope ya Labani, taonani, siinamuonekere iye monga kale.
3 Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe.
4 Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zake,
5 ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekere ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.
6 Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu.
7 Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa.
8 Akati chotero, Zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako, zoweta zonse zinabala zamathothomathotho; ndipo akati iye chotere, Zamipyololomipyololo zidzakhala malipiro ako, ziweto zonse zinabala mipyololomipyololo.
9 Chomwecho Mulungu anazichotsa zoweta za atate wanu, nandipatsa ine.
10 Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m’kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga.
11 Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m’kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano.
12 Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga: chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchitira iwe.
13 Ine ndine Mulungu wa ku Betele, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m’dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.
14 Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tili nalonso gawo kapena cholowa m’nyumba ya atate wathu?
15 Kodi satiyesa ife alendo? Chifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu.
16 Chifukwa kuti chuma chonse Mulungu anachichotsa kwa atate wathu ndi chathu ndi cha ana athu; tsono, zonse wakunenera iwe Mulungu, uchite.
17 Ndipo anauka Yakobo nakweza ana ake ndi akazi ake pangamira;
18 ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziona mu Padanaramu, kuti anke kwa Isaki atate wake ku dziko la Kanani.
19 Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zake: ndipo Rakele anabaaterafia atate wake.
20 Ndipo Yakobo anathawa kwa Labani Mwaramu mobisika, m’mene sanamuuze iye kuti analinkuthawa.
21 Ndipo anathawa iye ndi zonse anali nazo: ndipo anauka naoloka panyanja naloza nkhope yake iyang’anire kuphiri la Giliyadi.
Labani alondola wothawayo
22 Tsiku lachitatu anamuuza Labani kuti Yakobo wathawa.
23 Ndipo iye anatenga abale ake pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye paphiri la Giliyadi.
24 Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang’anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.
25 Ndipo Labani anakomana naye Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema wake m’phirimo: ndipo Labani ndi abale ake anamanga m’phiri la Giliyadi.
26 Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga aakazi, monga mikoli ya lupanga.
27 Wathawanji iwe mobisika, ndi kundichokera kuseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze?
28 Ndipo sunandiloleze ine ndimpsompsone ana anga aamuna ndi aakazi? Wapusa iwe pakuchita chotero.
29 M’dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang’anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.
30 Tsono ungakhale ukadamuka chifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga?
31 Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Chifukwa ndinaopa: chifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako aakazi.
32 Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang’anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.
33 Ndipo Labani analowa m’hema wa Yakobo, ndi m’hema wa Leya, ndi m’mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze. Ndipo anatuluka m’hema wa Leya nalowa m’hema wa Rakele.
34 Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa chokhalira cha ngamira, nakhala pamenepo. Ndipo Labani anafunafuna m’hema monse, koma sanawapeze.
35 Ndipo Rakele anati kwa atate wake, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; chifukwa zochitika pa akazi zili pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo.
36 Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndachimwa chiyani? Uchimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?
37 Pakuti wafunafuna monse ndili nazo, kodi wapeza chiyani pa zinthu za m’nyumba mwako? Tafika nacho apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri.
38 Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye.
39 Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; padzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana.
40 Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m’maso mwanga.
41 Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m’nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.
42 Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m’manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.
Labani apangana ndi Yakobo
43 Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzachitira ine chiyani lero kwa ana anga aakazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?
44 Tsopano tiyeni tipangane pangano, ine ndi iwe; likhale mboni pakati pa ine ndi iwe.
45 Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa.
46 Ndipo Yakobo anati kwa abale ake, Sonkhanitsani miyala; ndipo anasonkhanitsa miyala nakundika mulu: ndipo anadya pamulupo.
47 Ndipo Labani anatcha pamenepo Yegara-Sahaduta; koma Yakobo anatcha Galedi.
48 Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Chifukwa chake anatcha dzina lake, Galedi;
49 ndi Mizipa, chifukwa kuti anati, Yehova ayang’anire pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzake.
50 Ukasautsa ana anga aakazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; taonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako.
51 Ndipo Labani anati kwa Yakobo. Taona muluwu, taona choimiritsachi, ndachiimiritsa pakati pathu.
52 Muluwu ndiwo mboni, choimiritsachi ndicho mboni, kuti ine sindidzapitirira pa muluwu kunka kwa iwe, ndipo iwe sudzapitirira pa muluwu ndi pa choimiritsachi kudza kwa ine kuti tichitirane zoipa.
53 Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki.
54 Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.
55 M’mamawa Labani anauka nampsompsona ana ake aamuna ndi aakazi, nawadalitsa: ndipo Labani anachoka, nabwera kumalo kwake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/31-04a38507240ece77257e0133469f7fed.mp3?version_id=1068—