Categories
GENESIS

GENESIS 38

Yuda ndi Tamara

1 Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira.

2 Ndipo Yuda anaona kumeneko mwana wamkazi wa Mkanani dzina lake Suwa: ndipo anamtenga, nalowa kwa iye.

3 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Eri.

4 Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Onani.

5 Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibu pamene mkazi anambala iye.

6 Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wake woyamba mkazi, ndipo dzina lake ndilo Tamara.

7 Koma Eri mwana wake woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye.

8 Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumchitira mkazi zoyenera mphwake wa mwamuna wake, ndi kumuukitsira mkulu wako mbeu.

9 Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkulu wake.

10 Koma chimene iye anachita chinali choipa pamaso pa Yehova, ndipo anamupha iyenso.

11 Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m’nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m’nyumba ya atate wake.

12 Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu.

13 Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Taona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zake.

14 Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili panjira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake.

15 Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: chifukwa iye anabisa nkhope yake.

16 Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; chifukwa sanamdziwe kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine.

17 Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m’ziweto. Ndipo mkazi nati, Kodi udzandipatsa ine chikole mpaka ukatumiza?

18 Ndipo iye anati, Chikole chanji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi chingwe chako, ndi ndodo ili m’dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye.

19 Ndipo mkazi anauka nachoka, navula chofunda chake, navala zovala zamasiye zake.

20 Ndipo Yuda anatumiza kamwana kambuzi ndi dzanja la bwenzi lake Mwadulamu, kuti alandire chikole padzanja la mkazi; koma sanampeze iye.

21 Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.

22 Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeze mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.

23 Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeze iye.

24 Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto.

25 Pamene anamtulutsa iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wake kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang’anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi chingwe, ndi ndodo?

26 Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatse iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo.

27 Ndipo panali nthawi ya kubala kwake, taonani, amapasa anali m’mimba mwake.

28 Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anatulutsa dzanja; ndipo namwino anatenga chingwe chofiira namanga padzanja lake, kuti, Uyu anayamba kubadwa.

29 Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, taona, mbale wake anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziphothyolera wekha bwanji? Chifukwa chake dzina lake linatchedwa Perezi.

30 Ndipo pambuyo pake anabadwa mbale wake, amene anali ndi chingwe chofiira pamkono pake, dzina lake linatchedwa Zera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/38-5c3d37c0d60dba834cde2ff20e75a688.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *