Categories
GENESIS

GENESIS 48

Yakobo adalitsa ana a Yosefe

1 Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.

2 Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Israele anadzilimbitsa nakhala tsonga pakama.

3 Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m’dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,

4 Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakuchulukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao chikhalire.

5 Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m’dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.

6 Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awatche dzina la abale ao m’cholowa chao.

7 Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m’dziko la Kanani m’njira, itatsala nthawi yaing’ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).

8 Ndipo Israele anayang’ana ana aamuna a Yosefe, nati, Ndani awa?

9 Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.

10 Koma maso a Israele anali akhungu mu ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.

11 Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndiona nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.

12 Ndipo Yosefe anatulutsa iwo pakati pa maondo ake, nawerama ndi nkhope yake pansi.

13 Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efuremu m’dzanja lake lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m’dzanja lake lamanzere ku dzanja lamanja la Israele, nadza nao pafupi ndi iye.

14 Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pamutu wa Efuremu, amene ndiye wamng’ono, ndi dzanja lake lamanzere pamutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba.

15 Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pake anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isaki, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,

16 mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.

17 Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pamutu wa Efuremu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pamutu wa Efuremu ndi kuliika pamutu wa Manase.

18 Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pamutu wake.

19 Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.

20 Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase.

21 Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.

22 Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m’dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/48-2cf7bc2e7173c11ad315fc043dd9323d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *