Categories
EKSODO

EKSODO 2

Kubadwa kwa Mose

1 Ndipo anamuka munthu wa banja la Levi, natenga mwana wamkazi wa Levi.

2 Ndipo anaima mkaziyo, naona mwana wamwamuna; m’mene anamuona kuti ali wokoma, anam’bisa miyezi itatu.

3 Koma pamene sanathe kum’bisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m’mbali mwa mtsinje.

4 Ndipo mlongo wake anaima patali, adziwe chomwe adzamchitira.

5 Ndipo mwana wamkazi waFaraoanatsikira kukasamba m’mtsinje; ndipo atsikana ake anayendayenda m’mbali mwa mtsinje; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge.

6 Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri.

7 Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?

8 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amake wa mwanayo.

9 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa.

10 Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m’madzi.

11 Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu Mwejipito ali kukantha Muhebri, wa abale ake.

12 Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha Mwejipito, namfotsera mumchenga.

13 M’mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikumenyana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?

14 Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika.

15 Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m’dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.

16 Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana aakazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao.

17 Pamenepo anadza abusa nawapirikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao.

18 M’mene anafika kwa Reuwele atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero?

19 Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m’manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.

20 Ndipo anati kwa ana ake aakazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya.

21 Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora.

22 Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamutcha dzina lake Geresomo; pakuti anati, Ndakhala mlendo m’dziko la eni.

23 Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.

24 Ndipo Mulungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukirachipanganochake ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.

25 Ndipo Mulungu anapenya Aisraele, ndi Mulungu anadziwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/2-90f4e1f8f67f6d2dfd269f428923e43c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *