Categories
EKSODO

EKSODO 3

Kuitanidwa kwa Mose

1 Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m’tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.

2 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera m’chilangali chamoto chotuluka m’kati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, chitsamba chilikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho.

3 Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji.

4 Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m’kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.

5 Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.

6 Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang’ana Mulungu.

7 Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;

8 ndipo ndatsikira kuwalanditsa m’manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m’dziko lija akwere nalowe m’dziko labwino ndi lalikulu, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.

9 Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako.

10 Tiye tsopano, ndikutuma kwaFarao, kuti utulutse anthu anga, ana a Israele mu Ejipito.

11 Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele mu Ejipito?

12 Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.

13 Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israele, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nao chiyani?

14 Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.

15 Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwomibadwo.

16 Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani mu Ejipito;

17 ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m’mazunzo a Aejipito, kukulowezani m’dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.

18 Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m’chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.

19 Koma Ine ndidziwa kuti mfumu ya Aejipito siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ai.

20 Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aejipito ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka.

21 Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Ejipito; ndipo kudzakhala, pamene mutuluka simudzatuluka opanda kanthu;

22 koma mkazi yense adzafunse mnzake, ndi mlendo wokhala m’nyumba mwake, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolide, ndi zovala; ndipo mudzaveke nazo ana anu aamuna ndi aakazi; ndipo mudzafunkhe za Aejipito.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/3-5525bed4c5ed59506c9457c932d08062.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *