Chozizwitsa chachiwiri: Achule
1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwaFarao, nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.
2 Ndipo ukakana kuwalola amuke, taona, Ine ndidzapanda dziko lako lonse ndi achule;
3 ndipo m’mtsinjemo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m’nyumba mwako, ndi m’chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m’nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m’michembo yanu yootcheramo, ndi m’mbale zanu zoumbiramo.
4 Ndipo achule adzakwera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa anyamata ako onse.
5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, pamtsinje, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule padziko la Ejipito.
6 Ndipo Aroni anatambasula dzanja lake pamadzi a mu Ejipito; ndipo anakwera achule, nakuta dziko la Ejipito.
7 Ndipo alembi anachita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa achule padziko la Ejipito.
8 Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.
9 Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m’mtsinje mokha?
10 Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti muziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu.
11 Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m’mtsinje mokha.
12 Ndipo Mose ndi Aroni anatuluka kwa Farao; ndi Mose anafuulira kwa Yehova kunena za achule amene adawaika pa Farao.
13 Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nafa achulewo kuchokera m’zinyumba, ndi m’mabwalo, ndi m’minda.
14 Ndipo anawaola miulumiulu; ndi dziko linanunkha.
15 Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Chozizwitsa chachitatu: Nsabwe
16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m’dziko lonse la Ejipito.
17 Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m’dziko lonse la Ejipito.
18 Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoze; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.
19 Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Chozizwitsa chachinai: Mizaza
20 Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.
21 Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.
22 Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m’mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati padzikoli.
23 Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi.
24 Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m’nyumba ya Farao, ndi m’nyumba za anyamata ake, ndi m’dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo.
25 Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mukani, mphereni nsembe Mulungu wanu m’dzikomu.
26 Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu chonyansa cha Aejipito; taonani, ngati tikamphera nsembe chonyansa cha Aejipito pamaso pao sadzatiponya miyala kodi?
27 Timuke ulendo wa masiku atatu m’chipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe.
28 Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m’chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere.
29 Ndipo Mose anati, Onani, ndilikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.
30 Ndipo Mose anatuluka kwa Farao, napemba Yehova.
31 Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsale ndi umodzi wonse.
32 Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalole anthu amuke.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/8-9b52f839af4d661081537454e22a4ac2.mp3?version_id=1068—