Categories
EKSODO

EKSODO 15

Nyimbo yolemekeza Mulungu

1 Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti,

Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu;

kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja.

2 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga,

ndipo wakhala chipulumutso changa;

ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza;

ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.

3 Yehova ndiye wankhondo;

dzina lake ndiye Yehova.

4 Magaleta aFaraondi nkhondo yake anawaponya m’nyanja;

ndi akazembe ake osankhika anamira mu Nyanja Yofiira.

5 Nyanja inawamiza;

anamira mozama ngati mwala.

6 Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu,

dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.

7 Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira Inu;

mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu.

8 Ndipo ndi mpumo wa m’mphuno mwanu madzi anaunjikika,

mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu;

zozama zinalimba m’kati mwa nyanja.

9 Mdani anati,

Ndiwalondola, ndiwapeza,

ndidzagawa zofunkha;

ndidzakhuta nao mtima;

ndidzasolola lupanga langa,

dzanja langa lidzawaononga.

10 Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza;

anamira m’madzi aakulu ngati mtovu.

11 Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova?

Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera,

woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?

12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja,

nthaka inawameza.

13 Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola;

mwamphamvu yanu mudawalondolera

njira yakunka pokhala panu poyera.

14 Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira;

kuda mtima kwagwira anthu okhala mu Filistiya.

15 Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa;

agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu;

okhala mu Kanani onse asungunuka mtima.

16 Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera;

padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala;

kufikira apita anthu anu, Yehova,

kufikira apita anthu amene mudawaombola.

17 Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka paphiri la cholowa chanu,

pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova,

malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.

18 Yehova adzachita ufumu nthawi yonka muyaya.

19 Pakuti akavalo a Farao analowa m’nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m’nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja.

20 Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m’dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang’ombe.

21 Ndipo Miriyamu anawayankha,

Imbirani Yehova, pakuti wapambanatu;

kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja.

Madzi a ku Mara

22 Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m’chipululu cha Suri; nayenda m’chipululu masiku atatu, osapeza madzi.

23 Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a pa Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara.

24 Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa chiyani?

25 Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m’madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa;

26 ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.

27 Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi awiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamanga chigono chao pomwepo pamadziwo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/15-32bbeed59877acc9f6ceee96ed122791.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *