Malamulo khumi a Mulungu
1 Ndipo Mulungu ananena mau onse amenewa, nati,
2 Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.
3 Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.
4 Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi padziko.
5 Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
6 ndi kuwachitira chifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga.
7 Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.
8 Udzikumbukira tsiku laSabata, likhale lopatulika.
9 Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumaliza ntchito zako zonse;
10 koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iliyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m’mudzi mwako;
11 chifukwa m’masiku asanu ndi limodzi Yehova adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi zinthu zonse zili m’menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.
12 Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m’dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
13 Usaphe.
14 Usachite chigololo.
15 Usabe.
16 Usamnamizire mnzako.
17 Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.
18 Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.
19 Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe.
20 Ndipo Mose anati kwa anthu, Musaope; pakuti Mulungu wadza kukuyesani ndi kuti kumuopa Iye kukhale pamaso panu, kuti musachimwe
21 Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukulu kuli Mulungu.
Za mafano ndi guwa la nsembe
22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israele, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kuchokera kumwamba.
23 Musapange milungu yasilivaikhale pamodzi ndi Ine; musadzipangire milungu yagolide.
24 Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng’ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.
25 Ndipo ukandimangira guwa la nsembe lamiyala, usalimanga ndi miyala yosema; ukakwezapo chosemera chako, waliipsa.
26 Kapena usakwere ndi makwerero ku guwa langa la nsembe, kuti angaoneke maliseche ako pamenepo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/20-5bc76c8798dfd835401df4b93ae30dc7.mp3?version_id=1068—